KODI MULUNGU ALI NAWO UTHENGA WAPADERA WA NTHAWI YATHU INO

Ramoni Umashankar anabadwa mufuko la ansembe a chi Hindu la Bramini. Akali wamng'ono, akulu ake adamphunzitsa kuti iye anali mulungu, ndi kuti pofuna kuuzindikira umulungu wake iye anayenera kuchita utumiki wakudziletsa ndi kusinkhasinkha mwauzimu molingana ndi chipembedzo cha chi Hindu.

Ramoni anayamba kufufuza Baibulo ndi zomwe Khristu amanena. Iye nthawi zonse analemekeza Yesu chifukwa cha kuzichepetsa kwake, komano tsopano Ramoni anamva kuti Yesu ameneyu anazitchula yekha kuti analidi Mwana wa Mulungu. Iye anazindikira kuti Akhristu ambiri amaoneka kuti anali ndi mtendere umene zaka zambiri zakusinkhasinkha mwauzimu kunalephera kupereka. Komabe Ramoni anatsimikiza mtima kuti achipeze choonadi mu chipembedzo chake cha chi Hindu.

Koma kenaka iye anaonera kanema wa moyo wa Khristu. Kwa nthawi yoyamba iye anazindikira kuti Yesu nakumana nacho chizunzo ndi mantha monga munthu wina aliyense. M'mbuyomo iye ankaganiza kuti Yesu mwina anagwiritsa ntchito mphamvu yake ya umulungu kuti apulumuke ku kuwawa kwa kupachikidwa. Koma tsopano iye analephera kuufotokoza mtanda. Iye anadabwa; Zinatheka bwanji Yesu ameneyu kupyola chivuto ngati chimenechi - chifukwa chaanthu ochimwa?

Potsiriza kusinkhasinkha za imfa ya Khristu, Ramoni anakutidwa ndi chionetsero chotere cha chikondi. Iye anatsimikiza kusiya chi Bramini chosilirikacho ndi kupereka moyo wake kwa Yesu, Mpulumutsiyo. Poyerekeza ndi chikondi chodzipereka nsembe cha Yesu, Ramoni anati, "Zina zonse zinasanduka zopanda pake."

M'nyamata uyu wa chi Bramini anapeza chilikati chenicheni cha choonadi cha chikhristu: Yesu, Mpulumutsi wa dziko lonse lapansi.

1. NDI CHIPEMBEDZO CHITI CHOMWE CHIMAPULUMUTSA?

Yesu ndiye njira - njira yokhayo basi - ya chipulumutso.

"Ndipo palibe chipulumutso mwa wina yense, pakuti palibe dzina lina pansi pa thambo lakumwamba, lopatsidwa mwa anthu, limene tiyenera kupulumutsidwa nalo." - Machitidwe 4:12.

Baibulo limaphunzitsa momveka bwino kuti ife ndife otayika mu uchimo, ndi kuti motero taikika ku chilango cha uchimo: imfa (Aroma 6:23). Onse anachimwa (Aroma 3:23), chotero onse ayang'anana ndi imfa. Ndipo ndi Yesu yekha - Iye yekha basi- amene angatipulumutse ife ku kutsutsidwa kwa uchimo.

"Yense wakuyang'ana mwana, ndi kukhulupirira Iye, ali nawo moyo wosatha; ndipo Ine ndidzamuukitsa iye tsiku lomaliza." - Yohane 6:40.

Pali chipembedzo chimodzi chokha choona:
"Ambuye mmodzi, chikhulupiriro chimodzi, ubatizo umodzi." - Aefeso 4:5.

2. KODI MULUNGU ALI NAWO UTHENGA WAPADERA KWA AKHRISTU A M'MASIKU OMALIZA?

Inde. Uthenga uwu wa mbali zitatu umapezeka mu Chibvumbylutso 14:6-16. Kulalikidwa kwa mauthengawa kolalikidwa ndi angelo awa atatu kukumalizira ndi kudza kwachiwiri kwa Khristu (mavesi 14-16).

(1) Uthenga wa Mngelo Woyamba
"Ndipo ndinaona mngelo wina alikuuluka pakati pa mlengalenga, wakukhala nawo Uthenga Wabwino wosatha, aulalikire kwa iwo akukhala pa dziko, ndi kwa mtundu uli wonse ndi pfuko ndi manenedwe ndi anthu; ndi kunena ndi mau akuru, Opani Mulungu, Mpatseni ulemerero. Pakuti yafika nthawi ya chiweruziro chake; ndipo mlambireni Iye amene analenga m'mwamba ndi mtunda ndi nyanja ndi akasupe amadzi." - Chibvumbulutos 14:6, 7.

Ngakhale malembo Oyera akuonetsera mwachindunji mauthenga atatu awa kupyolera mu phiphiritso la angelo atatu, anthu a Mulungu ndiwo amene ali amithenga oulalikira uthenga ku dziko lonse lapansi. Iwotu sakulalikira uthenga wina watsopano , koma "Uthenga womwewo wosatha" ku dziko lonse lapansi - "Kwa mtundu uli wonse, ndi pfuko ndi manenedwe ndi anthu." Uthenga uwu wosatha" wa Yesu ndi uthenga womwewo wa chipulumutso womwe anthu a m'nthawi ya m'chipangano chakale anaulandira "mwa chikhulupiriro" (Ahebri 3:16-19; 4:2; 11:1-40); chiphunzitso chomwecho chimene Yesu Mwini anachilalikira; uthenga womwewo akuphunzira (aphunzi) anaulalikira pomgonjetsa Yesu dziko lapansi; uthenga womwewo umene wagwedeza dzikoli mu zaka mazana-mazana a nyengo ya chikhristu.

Uthengawu, wofewa ndi wa chindunji, wopulumutsa wa Yesu Khristu, udatsala pang'ono kuzimira kuchoka mu mpingo kwa zaka zoposera zikwi mu nthawi ya mdima, koma nthawi yakukonzanso inaubwezeranso, ndipo anthu a Mulungu akuulalikira ku dziko lonse lero. Mngelo woyambayu akulalikira uthenga wabwino womwewu, komano akuupereka mu chikhazikitso chatsopano - chakuta dziko lonse lapansi - kwa anthu omwe akukhala mmasiku oyang'anana ndi kudza kwa chiwiri kwa Yesu.

Iwo amene akuulandira uthengawu akudzipeza okha akuitanidwira ku "kuopa Mulungu ndi kumpatsa ulemerero (kuonetsera khalidwe Lake)". Iwo akulionetsera dziko lapansi khalidwe la Mulungu lachikondi, osati m'mau awo okha ai, komanso m'moyo wao wochitira umboni. Iwo akupereka chibvumbulutso chopatsa chidwi cha zomwe Mulungu angachite kudzera mwa anthu odzazidwa ndi Mzimu wa Khristu.

Kodi ndi nthawi iti imene mauthenga awa a angelo atatu ayenera kulalikidwa kudziko lonse lapansi? Ndi nthawi imene ola la "Chiweruziro cha Mulungu lafika." Phunziro 13 akufotokoza kuti Yesu anayamba ntchito ya chiweruziro chake chofufuza mu 1844. M'chaka chomwecho, 1844, Yesu anauzirira ndi Mzimu Wake anthu ambiri padziko lonse kuyamba kulalikira uthenga uwu wa m'Chibvumbulutso 14.

Uthenga umenewu ukutiitana ife tonse kuti "timulambire Iye amene analenga m'mwamba, (ndi) dziko" (Chibvumbulutso 14:7). Mulungu akutiitana ife tonse kuti "tizikumbukira tsiku la Sabata pakulisunga kuti likhale loyera" chifukwa "m'masiku asanu ndi limodzi Yehova adamaliza zakumwamba ndi zapansi (Eksodo 20:8-11). Mu chaka cha 1844 pamene Darwin anali kulenga ndi kuphunzitsa za chilengedwe kudzera mu kusinthasintha kwa zinthu, Mulungu naye anali kuitana anthu kuti azipembedza Iye monga Mlengi wao ndi wa zinthu zonse. Pa nthawi yokhayokhayi, iwo amene anali kulalikira mauthenga awa a angelo atatu, anapeza Sabata la tsiku lachisanu ndi chiwiri la m'Mau a Mulungu nayamba kulisunga pakufuna kulemekeza Mlengi wa kumwamba ndi dziko lapansi.

(2) Uthenga wa Mngelo Wachitatu
"Ndipo anatsata mngelo wina mnzake ndi kunene, Wagwa, wagwa Babulo waukulu umene unamwetsako mitundu yonse ku vinyo wa mkwiyo wa chigololo chake." - Chibvumbulutso 14:8.

Mngelo wachiwiriyu akuchenjeza "wagwa Babulo wamkulu" Chibvumbulotso 17 amaonetsera "Babulo" wauzimu - chikhristu chachipatuko - monga ngati mkazi wachigololo (vesi 5). Iye waima motsutsana ndi mkazi woyera wa m' Chibvumbulutso 12 amene akuimira mpingo woona wa chikhristu. Mkazi uyu yemwe akuimira Babulo ndi mkazi wakugwa yemwe "anamwetsako mitundu yonse ku vinyo wa mkwiyo wa chigololo chake" Vinyo wa chiphunzitso chonyenga walowerera mu ziphunzitso zonyenga zonse za chikhristu. Uthenga uwu wa mngelo wa chiwiri ukuitana anthu onse a Mulungu kuti akane ziphunzitso zonyengazi za chikhristu cha mpatukochi.

Babulo akuimira chisakanizo cha mitundu yambiri ya chikhristu champatuko. Iyeyu ndi woopsya kwambiri chifukwa amasokoneza ndi kukwiyakwiya chithunzi cha Mulungu ndipo chimaoneka ngati chipukwani chamafupa okhaokha: Mulungu motero amaoneka ngati wa nkhanza ndi wobwezera, kapena ngati gogo wokoma mtima molekerera kwambiri mwakuti sasamala ngakhale wina azichita uchimo. Mpingo woona ndi wanthanzi la umulungu udzaonetsera chithunzi cheni cheni cha makhalidwe onse a Mulungu pamodzai ndikuonetseranso mmene chilungamo chake ndi chifundo zimagwirizizirana ndi choonadi chakuti Mulungu ndiye chikondi.

Mulungu akuitana anthu kuti "atuluke mu Babulo" (Chibvumbulutso 18:4), pokana ziphunzitso zosachokera mu Baibulo ndi kutsata ziphunzitso za Khristu Yesu.

(3) Uthenga wa Mngelo Wachitatu
"Ndipo anawatsata mngelo wina, wachitatu, nanena ndi mau akulu, 'ngati wina alambira chilombocho, ndi fano lake, nalandira lemba pa mphumi pake, kapena padzanja lake, iyenso adzamwako ku vinyo wa mkwiyo wa Mulungu, wokonzeka wosasanganiza m'chikho cha mkwiyo wake; ndipo adzazunzika ndi moto ndi sulfure pamaso pa angelo oyera mtima ndi pamaso pa Mwanawankhosa, ndipo utsi wa kuzunza kwao ukwera ku nthawi, ndipo sapuma usana ndi usiku iwo akulambira chirombocho ndi fano lake, ndi iye ali yense akalandira lemba la dzina lake. Pano pali chipiliro cha oyera mtima, cha iwo akusunga malamulo a Mulungu, ndi chikhulupiriro cha Yesu." - Chibvumbulutso 14:9-12.

Uthenga wa mngelo wachitatuwu ukugawa dziko lonse m'magulu awiri. Ku mbali imodzi kuli Akristu a mpatuko omwe "amalambira chirombo ndi fano lake ndi kulandira lemba lake pamphumi kapena pa dxanja lawo." Ku mbali inayi kuli iwo amene amakana ulamuliro wa chirombo, "Oyera mtima" amene "amamvera malamulo a Mulungu ndi kukhala okhulupirika kwa Yesu."

Taonani kusiyana kumene kulipo pakati pa magulu awiri otsutsanawa. Iwo amene alandira lemba la chirombo ndi opembedza amene amagwetsa pansi mbendera za chi Khristu choona natsata ziphunzitso ndi nzeru za anthu zimene zimawakomera. "Oyera mtimawa" ali ndi chikhalidwe chowasiyanitsa ndi opandukawa. "Kupirira" kumvera malamulo a Mulungu, ndi "Kukhalabe okhulupirika kwa Yesu".

Mauthenga atatu ogwirizanawa atalalikidwa ku dziko lonse la pansi, Yesu adzabwera "Kudzakolola" opulumutsidwa.

"Ndipo ndinapenya, taonani, mtambo woyera' ndi pamtambo padzakhala wina monga Mwana wa munthu, wakukhala naye korona wa golidi pamutu pake, ndi m'dzanja lake zenga lakutwa. Ndipo mngelo wina anatuluka m'kachisi, wopfuula ndi mau akulu kwa Iye wakukhala pa mtambo. 'Tumiza zenga lako ndi kumweta, pakuti yafika nthawi yakumweta; popeza dzinthu dza dziko dzachetsa'. Ndipo iye wokhala pamtambo anaponya zenga lake padziko, ndipo dzinthu dza dziko dzinamwetedwa." - Chibvumbulutso 14:14-16.

3. MPINGO WA KHRISTU WA MMASIKU WOTSIRIZA

Kodi mudayamba mwamyamikira Mkhristu wamphamvu, wokhazikika, m'mudabwa kudzipereka, chipiriro ndi chikhulupiriro zomweanali nazo ndi kulakalaka kukhala nawo machitidwe auzimu monga akewo? Mulungu anapereka uthenga Wake wapadera wa m'masiku athu ano mu Chibvumbulutso 14 chifukwa iwo ungatulutse machitidwe a chikhalidwe ngati cha mkhristu ameneyu.

Monga kudafotokozedwa mu Phunziro 25, Chibvumbulutso 12:17 amazindikiritsa Akhristu am'masiku omaliza monga "iwo amene asunga malamulo a Mulungu, nakhala nawo umboni wa Yesu." Chibvumbulutso 14:12 akulifotokoza gulu lomweli monga "Oyera mtima amene asunga malamulo a Mulungu, ndi chikhulupiriro cha Yesu."

Tatiyeni timange pamodzi mwachidule makhalidwe awa a Akhristu a m'masiku omaliza.

(1) Iwo "ali nawo umboni wa Yesu"
Ngakhale pamene Satana awatulutsira ukali pa iwo, iwo "amakhalabe wokhulupirika kwa Yesu. "Chikhulupiriro chawo sichongodzipangira mwa iwo wokha ai, chili mphatso yochokera kwa Mulungu (Aefeso 2:8). Mpingo wa Mulungu wa m'masiku otsiriza udzimuona Yesu Khristu moonekera koposa mu chikhalidwe chake choona ndipo mwachisomo chodzera mu chikhulupiriro Akhristu ake a mpingowu azikhala monga zipilala za moyo zoonetsera mphamvu ya Khristu yokha mkati mwao.

(2) Iwo "asunga … chikhulupiriro cha Yesu" (Chibvumbulutso 14:12). Chikhulupiriro chimene Yesu anali nacho, chimene Iye adaphuzitsa, chikhulupiriro chimene Iye anachikhala m'moyo Wake, tsopano chidzaza m'mitima yawo. Iwo samangokhala nacho choonadi choka ai, "amasunganso" choonadi - amachitsatira. Kwa iwo chipembedzo ndiye moyo, chikhulupiriro chilamulira chikhalidwe ndi zochita zawo, ndipo chiphatikizana ndi kumvera. M'moyo wao watsiku ndi tsiku "chikhulupiriro cha Yesu" chionekera. Iwo apeza kuti ziphunzitso zazikulu za m'Baibulo zikagwiritsidwa ntchito m'myoyo wa tsiku ndi tsiku, zimatulutsa moyo wochitachita wa chikhristu. Iwo apeza kuti zoonadi zikuluzikulu za m'baibulo zimadzutsa chikondi ndi kudzipereke kwa Khristu komwe kumakwanitsa chosowa chilichonse ndi cholakalaka chilichonse cha mtima wake wa munthu.

(3) Iwo amasunga (amamvera) malamulo a Mulungu" - malamulo khumi, lamulo la chikhalidwe la Mulungu.

Koposa zonse iwo amafuna kumvera chifuniro chilichonse cha Mulungu, ndi lamulo lake lililonse. Iwo amaonetsa chikondi chawo kwa Mulungu ndi kwa anthu ena onse pakutsatira malamulo onse a Mulungu, kuphatikizapo lamulo lachinayi limene limatilangiza kupembedza Mlengi wathu pa kuyeretsa Loweruka, lomwe lili Sabata la tsiku lachisanu ndi chiwiri.

(4) Iwo amagawira ena "uthenga wabwino wosathawu" ku dziko lonse lapansi (Chibvumbulutso 14:6).
Uthengawu umanenetsa kuti Yesu adafera machimo athu, kenaka nkuuka kwa akufa kuti ife tikhale nawo machitidwe a chiyanjano cha chipulumutso ndi Iye. Mpingo wa Khristu wa m'masiku otsiriza wakhala ukuitanira anthu kulikonse kuti atuluke mu chisokonekero cha chipembedzo ndi kulumikizana ndi Yesu potsatira choonadi cha m'Baibulo mokha basi.

(5) Iwo amakhala ndi chikakamizo cha changu m'moyo wao chifukwa "yafika nthawi yakumweta; popeza dzinthu dza dziko adzachetsa" (Chibvumbulutso 14:15), ndipo miyanda miyanda ya anthu siinampezebe Khristu.

(6) Iwo atengeka ndi utumiki wopatsidwa ndi Mulungu. Chifukwa "Babulo wamkulu" akugwa, iwo akudandaulira anthu awo amene akukhalabe mu chipembedzo chosokonekeracho, "Tulukani m'menemo, anthu anga" (Chibvumbulutso 18:4). Iwo akufuna kugawana ndi aliyense chiyanjano chodabwitsa ndi chawo zimene ali zimene ali nazo mwa Khristu.

Izi zonse ndi zina zambiri zimalunzanitsa pamodzi mitima ya miyanda miyanda ya Akhristu a m'masiku otsiriza omwe adaitanidwa ndi mauthenga a angelo atatuwa. Moyo wawo wachimwemwe umawatsogolera iwo kulumikizana ndi mtundu Yohane pakukuitanani uku:

"Tikulalikirani inunso, kuti inunso mukayanjane pamodzi ndi ife; ndipo chiyanjano chathu chilinso ndi Atate, ndipo ndi Mwana wake Yesu Khristu; ndipo izi tilemba ife, kuti chimwemwe chathu chikwaniridwe." - 1 Yohane 1:3, 4.

Kudzera mwa Mzimu Wake ndi mwa mpingo Wake, Yesu akukuitanani inunso kuti mudze ndi kupereka zonse kwa Iye.

"Ndipo Mzimu ndi mkwatibwi anena, Idzani: Ndipo wakumva anene, 'Idzani' Ndipo wakumva ludzu adze; iye wofuna, atenge madzi a moyo kwaulere." - Chibvumbulutso 22:17.

4. MAKHOLOLA AWIRI

Mauthenga awa a angelo atatu afika kumapeto kwake pamene Yesu adzanso ku dziko lino kudzakolola opulumutsa a mibadwo yonse (Chibvumbulutso 14:14-16). Yesu asonkhanitsa opulumutsidwa onse nawatengera iwo ku "Malo okhalamo ambiri" Kumwamba (Yohane 14:1-3). Iye tsopano achotsa kwa nthawi zonse uchimo, matenda, zisoni ndi imfa. Oyera mtima tsopano ayamba kukhala miyoyo yawo yatsopano ndi Iye zaka zamuyaya (Chibvumbulutso 21:1-4).

Yesu "adzakololanso" oipa pakudza Kwake:
"Ndipo mngelo wina anatuluka m'Kachisi ali m'Mwamba, nakhala nalo zenga lakuthwa nayenso. Ndipo mngelo wina anatuluka pa guwa lansembe, ndiye wakukhala nawo ulamuliro pamoto; nafuula ndi mau akulu kwa iye wakukhala nalo zenga lakuthwa, nanena, Tumiza zenga lako lakuthwa, nudule matsango a munda wampesa wa m'dziko; pakuti mphesa zake zapsa ndithu. Ndipo mngelo anaponya zenga lake ku dziko, nadula mphesa za m'munda wa m'dziko, naziponya moponderamo mphesa mwamukulu mwa mkwiyo wa Mulungu. Ndipo moponderamo mphesa anamuponda kunja kwa mzinda,
ndipo mudatuluka mwazi moponderamo mphesa." - Chibvumbulutso 14:17-20.

Iyitu idzakhala nthawi yoopsya ya chionongeko chotsiriza chochitika chomvetsa chisoni kwa Khristu chifukwa Iye ayenera kuwaononga awo amene anakana kupulumutsidwa. Yesu "aleza mtima kwa inu, wosafuna kuti ena aonongeke, koma kuti onse afike kukulapa" (Petro 3:9).

Pamene Yesu akubwera kudzakolola khola la dziko, kodi inu mudzakhala mu kholola liti? Kodi mudzaima pakati pa tirigu wakucha pamodzi ndi oomboledwa a mibadwo yonse (Chibvumbulutso 14:13-16)? Kapena mudzakhala pakati pa mphesa zakucha zachionongeko pamodzi ndi otaika (mavesi 17-20)?

Nkhaniyitu yafotokozedwa momveka bwino. Ku mbali imodzi, Yesu waima atatambasula manja ake okhomedwa misomali, kukudandaulirani inu kuti mutenge mbali yanu pamodzi ndi "oyera mtima amene" asunga malamulo a Mulungu, ndi chikhulupiriro cha Yesu (vesi 12). Ku mbali inayi ku mau a anthu wamba, amene akunena motsindika kuti kumvera zonse za m'Baibulo ndi malamulo onse a Mulungu sizofunika kweni-kweni ai.

Chikhamu cha anthu m'bwalo loweruzira milandu la Pilato lidakhalanso ndi machitidwe okhaokhawa. Ku mbali imodzi kunali Yesu, Mulungu-munthu, Ku mbali inayi kunali Baraba, munthu wosowa chithandizo, yemwe sakadatha ngakhale kudzithandiza yekha kapena iwo a mu chikhamuchi amene ankachitira umboni zonsezi. Komabe pamene mau a ulamuliro a Pilato anamvekera ponseponse, "Ndi ndani wa awiri amene ndikumasulireni?" chimkokomo ca anthu wokwiya chidayankha, "Baraba"

"Nangano" adafunsa Pilato, "ndidzachita naye chiyani Yesu, wotchedwa Khristu?"

Mogwirizana, chikhamucho chidafuula, "Apachikidwe pa mtanda!" Motero Yesu, Wosachimwayo, adapachikidwa pa mtanda; ndipo Baraba, wopalamulayo, anamasulidwa (Onani Mateyu 27:20-26).

Nanga inu musankha yani lero, Baraba kapena Yesu? Kodi musankha kutsatira maganizo opangidwa ndi anthu ndi ziphunzitso zomwe zili zothutsana ndi malamulo a Mulungu ndi uthenga wosatha wa Yesu? Kapena mufuna "kumvera malamulo a Mulungu ndi kukhala okhulupirika kwa Yesu"? Kumbukirani, Yesu ndiye amene alonjeza kutumiza Mzimu Wake Woyera kuti akuthangateni mu chivuto chanu chili chonse, achize kusweka mtima kwanu, ndi kukwanitsa chokhumba chanu chilichonse.

 

© 2003 The Voice of Prophecy Radio Broadcast
Los Angeles, California, U.S.A.