KUMWAMBA NDIKO KWANU

Munthu wina dzina lake Marco Polo wa ku dziko la Venice anapita ulendo wa ku maiko a ku m'mawa. Iye pobwera kufika kwao anthu ankaganiza kuti wazungulira mutu - chifukwa amakamba za nkhani zodabwitsa.

Iye ankafotokoza kuti anaona m'mizinda ya siliva ndi golidi. Akuti anaonanso miyala ikuyaka moto; zobvala zoponyedwa pa malawi a moto koma osayaka; za njoka zikuluzikulu zotalika koposa 10 mamitala, zokhala ndi pakamwa poti zikhoza kumeza munthu. Anakambanso za kuti anaona mtedza waukulu-ukulu okula ngati mutu wa munthu ndi nkhani zina zambiri. Anthu amangogwa nkuseka pomva nkhani ngati izi. Ndipo patapita zaka zambiri Marco Polo anadwala kwambiri munthu wina wotumikira Mulungu anabwera kudzamuona ndipo anamuuza Marco kuti ayenera kulapa pa bodza lomwe wakhala akuwuza anthu asanatsikire kuli chete. Koma iye anayankha kuti "Zonse ndakhala ndikunena ndi zoona… Ndipo sindinanene ngakhale theka la zimene ndinaona."

Baibulo liri ndi zina zofanana ndi nkhani ngati imeneyi. Alembi a Baibulo poyang'ana kutsogolo m;masomphenya anafotokoza zochepa za zimene anaona. Iwo anaona zambiri m'Baibulo tipezamo zina za zinthu zina

1. KODI KUMWAMBA NDI MALODI ENIENI?

Yesu akukonza malo enieni a ife panopa kumwamba kwenikweni.

"Mtima wanu usavutike; mukhulupirira Mulungu, khulupirirani inenso (Yesu). Mnyumba ya atate wanga alimo malo okhalamo ambiri. Ngati sikudali kutero, ndikadakuuzani inu, pakuti NDIPITA KUKAKONZERA INU MALO. Ndipo ngati ndipita kukakonzera inu malo, NDIDZABWERANSO, ndipo ndidzalandira inu kwa Ine ndekha; kuti kumene kuli Ineko, mukakhale inunso." - Yohane 14:1-3.

Yesu akubweranso kachiwiri kudziko lino lapansi kudzatitengera kunyumba yokonzedweratu kumzinda woyera ndi waulemerero kumwamba, womwe sitingathe kuuganizira Yerusalemu watsopano. Titatha kukhala kumeneko zaka chikwi, Yesu akubweretsa mzindawo padziko lapansi pano. Ndiye pamene Yerusalemu watsopanoyu adzatsika, moto udzakhala utayeretsa dzikoli lonse. Dziko lathu lapansi lokonzedwanso mwatsopano lidzasandulika kwawo kwamuyaya kwa opulumutsidwawo. (Chibvumbulutso 20:7-15), izinso tizipeza zambiri mu phunziro la no. 25. Kodi Yohane, wolemba Chibvumbulutso, akuona zotsatiranso ziti?

"Ndipo ndinaona m'mwamba mwatsopano ndi dziko latsopano; pakuti m'mwamba moyamba ndi dziko loyamba zidachoka, ndipo kulibenso nyanja. Ndipo ndinaona mzinda woyerawo, Yerusalemu watsopano, ulikutsika kumwamba kwa Mulungu, wokonzeka ngati mkwatibwi wokometsedwera mwamuna wake. Ndipo ndinamva mau akuru ochokera ku mpando wachifumu ndi kunena Taonani Chihema cha Mulungu Chiri mwa anthu; ndipo adzakhalitsa nao, ndi iwo adzakhala anthu ache ndi Mulungu yekha adzakhala nao, Mulungu wao." - Chibvumulutso 21:1-3.

Ndani adzalandire dziko lapansi losandulika?

"Odala ali akufatsa; chifukwa adzalandira dziko lapansi." - Mateyu 5:5 (Onaninso Chibvumbulutso 21:7).

Yesu akulonjeza adzabweranso dziko latsopano lokongola ngati Edeni wakaleyo, ndi anthu "Ofatsa adzalandira dziko lapansi".

2. KODI KUMWAMBA TIDZAKHALA NDI MATUPI ATHU OMWEWA?

Kodi pamene Yesu nauka m'manda naonekera kwa ophunzira ake, anati chiani za thupi lake?

"Onani manja ndi mapazi anga, ndine amene ndikuuzeni ndipo onani; mzimu sukhala ndi thupi ndi mafupa, monga mundionera Inemu." - Luka 24:39.

Yesu anali ndi thupi leni-leni ndipo anamuuza Tomasi kuti amukhudze (Yohane 20:27) pa nthawi iyi nkuti Yesu nalowa m'nyumba yeni-yeni ndipo anayankhula ndi anthu eni-eni; nadya chakudya ndithu (Luka 24:43).

Kumwamba sikudzakhala mizimu koma anthu eni-eni amene amakondwera ndi moyo wauzimu koma matupi adzakhala ovala ulemerero.

"Pakuti ufulu wathu uli kumwamba, kuchokera komweko tilindira mpulumutsi, Ambuye Yesu Khristu; amene adzasanduliza thupi lathu lopepulidwa, lifanane nalo thupi lake la ulemerero, monga mwa machitidwe amene akhoza kudzigonjetsera nao zinthu zonse." - Afilipi 3:20, 21.

Inde matupi athu, monga thupi la Yesu poukitsidwa, lidzakhala leni-leni. Kodi nanga tidzawadziwa abale ndi abwenzi athu kumwamba? Inde.

"Pakuti tsopano tipenya m'kalirole, ngati chimbuuzi; koma pomwepo maso ndi maso tsopano kuzindikira mderamdera, koma pomwepo ndidzazindikiratu, monganso ndazindikiridwa." - 1 Akorinto 13:12.

Kumwamba tidzadziwadi zambiri tidzadziwa zakuya ndipo tidzayamika Mlengi. Ophunzira adalizindikira thupi laulemerero la Yesu (Luka 24:36-43). Mariya adadziwa Yesu pa tsiku louka kumanda chifukwa cha mau ake a Yesu (Yohane 20:14-16).

Ophunzira a Yesu pa njira ya ku Emau anamzindikira Yesu pamene Iye anapempherera chakudya (Luka 24:13-35). Oomboledwa adzaonana maso ndi maso ndi anzao! Kumwetulira kwa amuna anu, kaya akazi anu, amene namwalira mudzakuzindikira! Mudzawadziwa ana anu amene anamwalira kale pokumbukira zimene amachita ali ndi moyo pa dziko lapansi. Inde ngakhale abwenzi anu okondedwa mudzawadziwa! Inde kudzakhala chisangalalo chosatha!

3. KODI TIDZIDZACHITANJI KUMWAMBA?

Tidzakhala ndi zobetchera kumwamba? Kodi padzafunika kuganiza kumanga nyumba zathu zathu?

"Tamverani! Taonani, ndilenga kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano… ndidzasangalala mu Yerusalemu ndi anthu anga… adzamanga nyumba ndikukhalamo, adzabvala ndi kudya zipatso zake… anthu anga adzasangalala ndi ntchito ya manja ao." - Yesaya 65:17-22.

Yesu akutikonzera malo kumwamba aliyense payekha payekha - mu mzinda watsopano wa Yerusalemu (Yohane 14:1-3, Chibvumbulutso 21). Mavesi awa amatiuza kuti tidzamanga nyumba zokongola. Inde zoposa zimene timaziona lero ku mayadi.

Kodi mumakonda kuona mathithi a madzi kapena mumakonda nkhalango zokongola? Imvani izi:

"Yehova watonthoza mtima wa ziyoni, watonthoza mtima wa malo ake onse abwinja, ndipo wasandutsa chipululu chake ngati Edene…" - Yesaya 51:3.

Mulungu adzalitembenuza dziko kuti lioneke monga Edene wakaleyo. Sikudzakhalanso matope m'miseu yake, ngakhale nyansi zochokera m'mafakitole.

Udzakhala ngati m'banda kucha watsopano poona dziko latsopano-anthu a Mulungu adzakhalamo kwa muyaya.

Kodi mumakonda zinthu zatsopano? Maphuziro? Kapena kuyambitsa zinthu zatsopano? Tamvani izi: "Maganizo mwa anthu oomboledwa mudzalowa mphamvu yoti adzamve zinthu za Umulungu… maganizo ndi malingaliro adzakula … Tidzaphuzira maphunziro a nthano ya maomboledwe". - Great Controversy page 677, Ellen White.

4. KODI UCHIMO UDZAOPSEZANSO ANTHU OOMBOLEDWA?

"Ndipo simudzalowanso konse momwemo kanthu kali konse kosapatulidwa kapena iye wakuchita chonyansa ndi bodza; koma iwo okha olembedwa m'bukhu la moyo la mwana wa nkhosa." - Chibvumbulutso 21:27.

Mulungu ali wokonzeka kuthana ndi uchimo ndi zotsatira zake! Yesu akadzaoneka m'mitambo tidzamuona Iye (1 Yohane 3:2). Tidzatsatira chiyero osati kukhunba kupha, bodza ndi chigololo.

"(Mulungu) ndipo adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pao, ndipo sipadzakhalanso imfa: ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa, zoyambazo zapita." - Chibvumbulutso 21:4.

Ngakhale, mdani wathu wotsiriza, imfa idzakhonjetsedwa uko kumwamba anthu sadzafa (1 Akorinto 15:53) palibe ati adzakalambe!

Kumwamba sikudzakhalanso olumala zoyamba za m'dziko loipali zidzapita kwa muyaya!

"Pamenepo maso a akhungu adzatsegulidwa ndi makutu a ogontha adzatsegulidwa. Pamenepo wopunduka adzatumpha ngati nswala, ndi lilime la wosalankhula lidzayimba pakuti chipululu madzi adzatuluka." - Yesaya 35:5, 6.

5. KODI CHOKONDWERETSA KOPOSA CHIDZAKHALA CHIANI KUMWAMBA?

Inde, kuonana ndi Mwini, Mbuye wa dziko lonse lapansi, chidzakhala chimwemwe choposa.

"Ndipo ndinamva mau akuru ochokera ku mpando wachifumu ndi kunena, Taonani, Chihema cha Mulungu chiri mwa anthu, ndipo adzakhalitsa nao, ndipo adzakhala anthu ake, ndipo Mulungu yekha adzakhala nao, Mulungu wao." - Chibvumbulutso 21:3.

Mulungu wamphamvu akulonjeza kuti adzakhala nafe ndi adzakhala Mphunzitsi wathu. Taganizani zidzakhala zokoma motani! Ngati mwachitsanzo woyimba nyimbo afika pamaso mwini wopeka nyimbo!

"Ndipo kudzakhala kuti kuyambira pa mwezi wokhala kufikira pa unzake, ndipo kuyambira pa Sabata lina kufikira pa linzake, anthu onse adzafika kudzapembedza pamaso pa Ine, ati Yehova." - Yesaya 66:23.

Pakati penipeni pa mzinda woyera pali mpando wachifumu wa Mulungu. Nkhope yozingidwa ndi utawaleza, anthu oomboledwa amasonkhana kupembedza Mulungu. Baibulo likuti.

"Ndipo oomboledwa a Yehova adzabwera nadzafika ku Ziyoni alikuimba; kukondwa kosatha kudzakhala pamitu yao, iwo adzakhala ndi kukondwa, ndipo chisoni ndi kuusa moyo kudzachoka." - Yesaya 35:10.

Nayu wina yemwe ukoma wake siutha. Iye ndiwokhulupirika ndiponso wopirira kosatha - lilemekezedwe dzina lake!

6. TIYENI TIKAPEZEKE KUMENEKO

Yesu akulakalaka kudzakomana ndi oomboledwa ake maso ndi maso. Nchifukwa chake analola kulipira dipo lalikuru pa mtanda. Inu mulandire nsembe iyi ndikubvomera kuti Yesu ndiye Mpulumutsi wanu, landirani chikhululukiro chochokera ku mtanda wa Yesu.

"Ndipo simudzalowa konse momwemo kanthu kali konse kosapatulidwa kapena iye wakuchita chonyasa ndi bodza; koma iwo okha olembedwa m'bukhu la moyo la Mwana wankhosa." - Chibvumbulutso 21:27.

Yesu amatiombola ku machimo osati mu machimo. Tiyenera ife kufika kwa Iye kudzera m'mphamvu zake. Iye ndiye mau a pakamwa pathu mpakana akadza!

Ufumu wa Mulungu ukhoza kuyambira mu mtima mwanu. Yesu akatimasula ku uchimo, mu mtima mwathu mumakhala mtendere wa kumwamba. Kafukufuku wa posachedwa anaonetsa kuti anthu amene amakhala mu chiyembekezo cha Yehova amakhala moyo wokondwa kuposa anzao.

Palibe china chingakupangeni inu kukhala wokondwa kuposa kudalira mwa Mulungu. Tamvani zomwe Petro akunena za chikhulupiriro. Amene ngakhale simunamuona mumkonda, amene ngakhale simunampenya tsopano, pokhulupirira, ndi cha ulemerelo ndi kulandira chitsiriziro cha chikhulupiriro chanu, ndicho chipulumutso cha moyo wanu (1 Petro 1:8, 9).

Iyi ndiye mphotho yomwe Ambuye watikonzera kodi mukuona moyo waulere mwa Yesu! Mukumva kuitana kwake?

Ndipo Mzimu ndi mkwatibwi anena, Idzani. Ndipo wakumva anene Idzani. Ndipo wakumva ludzu adze, iye wakufuna, atenge madzi amoyo kwaulere (Chibvumbulutso 22:17).

Yesutu ali nanu tsopano, ndipo akulankhula ndi inu pamene mukuwerenga mau awa. Akukuitanani akuti, Idzani idzani, idzani! Inde akukulindirani! Ino ndiyo nthawi yabwino yomulandira!

Bwanji osamuuza kuti mukulandira mphatso yomwe Iye akupereka ndipo kuti mufuna kukakhala naye muyaya? Muuzeni kuti mumukonda! Mthokozeni pa zimene wakuchitirani ndi zomwe wakukonzerani kuti akuchitireni! kodi pali china chotchinga pakati pa inu ndi Iye? Chichotseni! Lero pamene mukumva mau ake, dziperekeni kwa Iye, weramitsani nkhope yanu ndikupemphera kuti, Yesu Mbuye wanga ndibwera, ndikupatsani zonse. Ndikhale wanu nthawi zonse!

 

© 2003 The Voice of Prophecy Radio Broadcast
Los Angeles, California, U.S.A.