MWAYI WOKHALA MOYO WA CHIWIRI

Munthu wina wokalamba atatha kukhala moyo wake wonse m'chipembedzo cha chi Buda, nasankha kukhala mkhristu ku dziko la Singapore, anafunsidwa, "kodi inu Mr. Lim, mukupeza kusiyana kwa mtundu wanji pakukhala mkhristu ndi kukhala m'Buda?

"Ndikosavuta," anayankha choncho. "kuyambira pomwe ndinapeza Yesu ngati mpulumutsi wanga ndiri ndi mtendere waukuru mu mtima. Izi ndi zomwe zimachitika tikaika moyo wathu pa Khristu.

"Inu (Mulungu) mudzasunga mtima wokhazikika mu mtendere weni-weni chifukwa ndikhulupilirani inu," - Yesaya 26:3.

Kukhala moyo wachikhristu kumadzetsa mtendere wangwiro - kumva chitetezo chokhala bwino ndi changwiro. Iwo amene apeza chisangalalochi angopezeratu njira yokhayo ya ku mwayi wokhala moyo wachiwiri - Yesu!

1. TANTHAUZO LA KUPULUMUTSIDWA KWA IWO WOTAIKA

Nzotheka kuti munthu wa moyo wake wathanzi kukhala ndi moyo ndi nthawi yomwe ena angaitchule kuti ndiyabwino, koma ali wakufa - kufa kuuzimu.

"NDIPO INU, ANAKUPATSANI MOYO, pokhala munali akufa ndi zolakwa, zimene munayendamo kale, monga mwamayendedwe a dziko lapansi lino, monga mwa mkuru wa ulamuliro wa mlenga-lenga, wa mzimu wakuchita tsopano mwa ana a kusamvera." - Aefeso 2:1, 2.

Satana amatsogolera munthu wakufa muuzimu kuti agwebe mu uchimo ndi kusamvera. Koma choonadi chozizwitsa cha uthenga wabwino ndichakuti Mulungu amawakonda anthu oterewa. Iye amawakonda anthuwa adakali chichimwire, nawapatsa chipulumutso chaulele ndi chodzaza ku machimo awo.

"Chifukwa cha chikondi chake chakuya chimene anatikonda nacho, Mulungu, wodzala ndi chifundo, tingakhale tinali akufa m'zolakwa zathu, anatipatsa moyo pamodzi ndi khristu (muli opulumutsidwa mwa chisomo)… kuti akaonetsere m'nyengo zirinkudza chuma choposa cha chisomo chake, m'kukoma mtima kwa pa ife mwa Khristu Yesu." - Aefeso 2:4-7.

Mulungu anatikonda ngakhale pamene sitinali woyenera kukondedwa. Chisomo chake chinalenga m'miyoyo yathu, moyo watsopano wa khristu. Sitingathe kuzisintha tokha ayi, koma Mulungu akhoza. Tikabwera kwa Iye ndi chikhulupiliro ndi kudzipereka, amatipatsa ife mwayi wina wachiwiri ngati mphatso yaulele pa moyo wathu.

2. TIYENERA KUPULUMUTSIDWA KU CHIYANI?

(1) Tiyenera kupulumutsidwa ku tchimo.

"Pakuti onse anachimwa, naperewera pa ulemelero wa Mulungu." - Aroma 3:23.

Kunena mwachuchuchu, ife sitikhala moyo umene tinafunikira mwa ubwino. Kholo litha kupsa mtima ndi kum'pweteka mwana wake chifukwa mavuto ambiri Omwe avutitsa m'moyo wake. Munthu atha kukhala ndi chidwi pa woyendetsa galimoto mpaka kutsala pang'ono kuchita ngozi. Ophunzira atha kukhala wosathandizika nanena mau oipa pa za ophunzira mzake. Wochita malonda atha kukonza "kuti aiwale" za komwe kuchokera chuma chake nthawi ya msonkho. "Onse anachimwa," ndiye momwe munthu aliri m'menemo.

Kodi baibulo likutanthauzira bwanji tchimo?

"Chosalungama chiri chonse chiri uchimo," - 1 Yohane 5:17.

Tiyenera ife kupulumutsidwa ku makhalidwe onse oipa, monga bodza, mkwiyo woononga, zilakolako, kupsa mtima, pongonena zochepa.

"Yense wakuchita chimo achitanso kusaweruzika." - 1 Yohane 3:4.

Choncho tiyenera kupulumutsidwa ku tchimo loswa Malamulo ake a Yehova.

(2) Tiyenera kupulumutsidwa ku ubale wosweka umene ulipo ndi Mulungu.

"Koma zoipa zanu zokulekanitsani inu ndi Mulungu wanu; ndipo machimo anu abisa nkhope yake kwa inu kuti Iye sakumva." - Yesaya 59:2.

Tchimo lomwe silinakhululukildwe limachotsa ubale ndi Mulungu. Khristu anadza kudzabwezera chikhulupiliro mwa Mulungu, chimene satana anachisokoneza kuchichepetsa.

(3) Tiyenera kupulumutsidwa ku imfa yosatha chilango cha -mphotho ya utchimo.

"Chifukwa chake, monga uchimo unalowa m'dziko lapansi mwa munthu m'modzi, ndi imfa mwa uchimo, chotero imfa inafikira anthu onse, chifukwa kuti onse anachimwa." - Aroma 5:12.

(4) Tiyenera Kupulumutsidwa kumoyo wosakondwa, wopanda pache wa uchimo.

Kwa ochimwa, moyo ndi njira yokathera ku imfa basi.

(5) Ife tiyenera kupulumutsidwa ku dziko lodzala ndi uchimoli ndi zotsatira zake za machimowo-monga kukhala wosangalala, kusweka mtima, kukhala pa uwekha, nkhondo, matenda ndi imfa!

3. ANGATIPULUMUTSE NDANI?

(1) Yesu angatiombole ife ku tchimo.
"Ndipo udzamutcha dzina lake Yesu, pakuti iyeyu adzapulumutsa anthu ache ku machimo awo." - Mateyu 1:21.

Munthu wina wa chi Hindu anauza mzake wa chikhristu, "ndapeza zinthu zina zambiri mu chi Hindu zomwe sizipezeka mu chikhristu, koma pali chinthu chimodzi m'chikhristu chomwe mu chi Hindu mulibe. Ichi ndi Mpulumutsi.

Chikhristu ndi chipembedzo chokhacho m'dziko lapansi chomwe chimapereka kwa anthu Mpulumutsi.

(2) Yesu atha kutipulumutsa ku ubale wathu womwe udasweka ndi Mulungu.
"Kuti nthawi ija munali opanda Khristu… opanda chiyembekezo, ndi opanda Mulungu m'dziko lapansi. Koma tsopano mwa Yesu Khristu inu amene munali kutali kale, anakusendezani mukhale pafupi m'mwazi wa Khristu." - Aefeso 2:12, 13.

Yesu ndiye bwenzi langwiro yemwe tingakhale naye mu ubale wa chisangalalo.

Anakonda kutibweretsera ife zabwino zokha-zokha. "Kupyolera m'mwazi wa Khristu"moyo wathu wakale wamachimo unakhululukidwa, ndipo tsiku ndi tsiku amatilandira ndi kutivomereza ife kutipatsa moyo wake wangwiro. Tikudziwa kuti alipo nthawi zonse kutidzutsa pamene tagwa. Chikondi chathu paiye chimatsatira pobwera chikhumbo-khumbo chokhala mu njira yom'kondweretsa Iye.

(3) Yesu atha kutipulumutsa ku imfa ya muyaya yomwe ndi mphotho yache ya uchimo.
"Pakuti mphotho yake ya uchimo ndi imfa; koma mphatso yaulele ya Mulungu ndiyo moyo wosatha wa mwa Khristu Yesu Ambuye wathu." - Aroma 6:23.

Ife ndife oswa lamulo oyenera imfa. Mphotho ya uchimo ndi imfa. Yesu anatipulumutsa ife ku imfa yamuyaya natipatsa ife moyo wosatha.

"Koma Mulungu atsimikiza kwa ife chikondi chake kwa chikondi chake cha mwini yekha, m'menemo kuti pokhala ife chikhalire ochimwa, Khristu adatifera ife." - Aroma 5:8.

Chifukwa cha chikondi chosalephera, Yesu "anatifera ife." Ndiponso chifukwa anatifera ife nazunzidwa ndi mphotho yonse ya tchimo, Mulungu atha tsopano kukhululuka ndi kulandira wochimwa popanda kuchepetsa tchimolo.

(4)Yesu angatipulumutse ife ku moyo wosakondwa, wauchimo.
"Chifukwa chake ngati munthu ali yense ali mwa Khristu, ali wolengedwa watsopano, zinthu zakale zapita, taonani zakhala zatsopano." - 2 Akorinto 5:17.

Sitingathe ife kudzipulumutsa ife kudzipulumutsa tokha ku tchimo kapena kudzisintha tokha monga m'mene sizingakhalire zotheka mkango kusanduka khoswe (Aroma 7:18). Tchimo ndi lamphamvu kuposa maganizo athu. Koma Khristu atha kulimbikitsa inu ndi mphamvu mwa Mzimu wake mwa inu" (Aefeso 3:16). Iye amagwira ntchito yobwezera moyo wake wabwino m'malo amene khalidwe lathu linaonongeka; khalidwe labwinolo ndilo chikondi, mtendere, chisangalalo, chifatso ndi kudziletsa (Agalatiya 5:22, 23). Khristu amakhala moyo wake wonse mwa ife, ndipo timalandira machiritso a uzimu kubwezeretsedwanso mwatsopano ndi moyo watsopano.

Munthu wina wotchedwa Harold Hughes anataya chikhulupiliro chake kuti iye angathe kukhala wosinthika. Anayesa kusiya uchidakwa kwa nthawi yaitali koma analephera. Anaona kuti uchidakwa wake wazunzitsa mkazi ndi ana ake kwa zaka khumi. Ndiye tsiku lina analowa mu bafa losambira natenga mfuti yake nazilozetsa nayo mkamwa mwake.

Asanailole kuti imuombere, anaganiza zomulongosolera kaye Mulungu vuto lakeli. Pemphero lakeli linasandulika kudandaulira kolira kwakutali, kulilira chithandizo. Ndipo Mulungu anabwera. Harold Hughes anapanga chitsimikizo chake ndi Khristu napeza mphamvu za uzimu zomwe zinamuthandiza kupilira. Anasiiratu moyo wauchidakwa, nasandulika bambo wachikondi, ndi wodalirika ku banja lake ndipo anapeza mpando wa udindo mu nyumba ya Malamulo ya "Senate." Harold Hughes anapeza mphamvu yoposa zonse yakumusintha munthu m'dziko lino lapansi - ndiyo Yesu!

(5) Yesu angatipulumutse ku dziko la uchimo.
Mitu ya maphunzizro athu a kupeza mwatsopano anayi otsatirawa adzatifotokozera m'mene Yesu amapulumutsira anthu ku dziko lauchimo.

4. TIMAPULUMUTSIDWA NGATI TITHA KUCHITA ZINTHU ZITATU ZOSAVUTA IZI

(1) Kumufunsa Khristu kuthana ndi tchimo liri m'moyo mwathu.
Kodi ife mbali yathu ndiyotani pakuchotsa moyo wathu wauchimo?

"Lapani, bwelerani kuti afafanizidwe machimo anu." - Machitidwe 3:19.

"UBWINO WA MULUNGU UKUBWEZERA KUTI ULAPE." - Aroma 2:4.

"MWAMVETSEDWA CHISONI KU KUTEMBENUKA MTIMA." - 2 Akorinto 7:9.

Kulapa ndiko kumva chisoni ndi moyo wathu wakale wauchimo, ndikutembenuka mtima kuchoka ku chimolo; kusiya makhalidwe onse akale, ndi maganizo akale. Sichisoni chifukwa chongoopa chilango ayi, koma yankho lathu la kwa Mulungu ndi chifundo chake,' chomwe chinatsogolera Yesu kufa m'malo mwathu chifukwa cha machimo athu. Timakana tchimo chifukwa limamupweteka Mulungu.

Tikapeza moyo watsopano mwa Yesu Khristu, tiyenera kuyesetsa kusiya zonse zakale zoipa (Ezekiel 33:14-16).

Kodi ndi mbali yanji yomwe Mulungu ali nayo kuichita pochotsa moyo wathu wakale wauchimo?

Kulapa ndi kukhululukidwa; zonsezi ndi mphatso za Mulungu kwa ife.

"Ameneyo Mulungu anamkweza ndi dzanja lace lamanja, akhale mtsogoleri ndi MPULUMUTSI, kuti apatse kwa Israyeli KULAPA, ndi CHIKHULUPILIRO CHA MACHIMO." - Machitidwe 5:31.

Ndipo tikalapa, mpulumutsi wokondayo amatikhululukira machimo athu, natiyeretsa ife kumachimowo nawaponya kunyanja yakuya.

"NGATI TIVOMEREZA MACHIMO ATHU, ALI WOKHULUPILIKA NDI WOLUNGAMA IYE, KUTI ATIKHULULUKIRE machimo anthu ndi KUTISAMBITSA Chosalungama chonse." - 1 Yohane 1:9. (Onaninso pa Mika 7:18, 19.)

Palibe tchimo loopsa loti Mpulumutsi yemwe anafera machimo athu pa mtanda wa Karavali sangathe kukhululukira. Munthu amene akhulupilira mwa Yesu angofunika kumufunsa Iye, Yesuyo kuti amukhululukire. Kufa kwa Yesu, kufera ife sikungatipulumutse pamene ife sitinapemphe ayi. Ndizosakaikitsa kuti machimo athu ndiwo adapangitsa misomali ija kuboola thupi lake la Khristu paja pa mtanda, m'manja ndi m'mapazi ake.

Komabe Yesu akufunitsitsa, koposa m'mene tingaganizire kuti ife tilandire mphatso yakeyi ya kukhululukidwa ndi chiyanjano mwa iye.

Mawu adamufikira m'nyamata wina, yemwe adathawa kunyumba kwawo, kuti mayi ake ali pafupi kufa. Nkhaniyi inamuchititsa chisoni kwambiri poonanso ubale wake wosweka ndi banjali. Akufulumira kupita kunyumbako, anakadzigwetsa m'chipinda pa kama pomwe panagona mayi akewo ndi misozi, akulira mopempha kuti mayi akewo amukhululukire.

Mayi adamusendeza iye pafupi nawo namunong'oneza mawu awa, "mwana wanga, ndikadakhala nditakukhululukira kale ukadandipempha kotero."

Ngati inu mwapita kutali ndi Mulungu - Kapena simunamudziwebe - chonde, ganizirani momwe Iye aliri ndi chidwi chokulandirani ngati Atate wokonda akufunitsitsa ndithu koposa zonse kuti inu mulandire mphatso yake yakukhululukira. Yesu amakukondani. Anafera inu. Ali wolola nthawi zonse kukukhululukirani choncho, inunso muvomereni ku kuitanira ku kulapa kwake. Lapani machimo anu. Mungokhulupira basi kuti Mulungu akukhululukirani ndipo achitadi. Mkhulupirireni Iye! Khulupilirani malonjezo ake.

(2) Landirani moyo watsopano kuchokera mwa Yesu.
Mbali yanu polandira moyo watsopano kuchokera kwa Yesu ndikungokhupilira basi kuti Yesu wakupulumutsani inu. Vomerani popanda kung'ung'udza mfundo yoti Iye wakukhululukirani, ndikukuyeretsani, kutenga zonse zanu zakale zauchimo, ndikukupatsani moyo wonse weni-weni watsopano wosinthika.

"Koma onse… okhulipilira dzina lake, kwa iwo anapatsa (mphamvu, undindo, mwayi) wakukhala ana a Mulungu." - Yohane 1:12.

Monga mwana wa Mulungu, muli ndi "ufulu" wakulandira moyo watsopano kuchokera kwa Yesu. Monga tanena kale, simungathe inu kuchita izi mwa inu nokha - izi ndi mphatso yochokera kwa atate wanu wakumwamba! Yesu amapereka lonjezano leni-leni ili kuti akatichotsere ife mantha akusoweka chitetezo ndi kukaika.

Kodi Mulungu amachitapo mbali yanji potipatsa ife moyo watsopano?

"Yesu anayankha nati; "Indetu indetu ndinena ndi iwe, ngati munthu sabadwa mwatsopano, sakhoza kuona ufumu wa Mulungu." - Yohane 3:3.

M'malingaliro a Yesu, wochimwa wokhulupilira ndikulapa ali wobadwanso mwatsopano m'moyo. Ndichozizwa chomwe angachichite ndi Mulungu yekha basi. Iye akulonjeza:

"Ndipo ndidzakupatsani MTIMA WATSOPANO, ndi kulonga mkati mwanu MZIMU WATSOPANO, ndipo ndidzachotsa mtima wamwala m'thupi, ndikukupatsani mtima wamnofu." - Ezekiel 36:26.

Yesu amasintha mitima yathu - maganizo ndimakhalidwe athu - ndipo amakhala "mwa ife" (Akolose 1:27). Moyo watsopanowu siwodzala ndi zabwino zokha-zokha zauzimu ayi, ndiwovuta, kuuka kuchoka ku imfa yauzimu kunka ku moyo wonse watsopano ndi kukhala munthu wokhalako weni-weni.

(3) Moyo wa chikhristu umafuna tsiku liri lonse kumachoka ku kudzikonda, ndikulumikizana ndi Yesu bwenzi lathu lokonda. Timakula m'moyo watsopanawo pakulimbikitsa ubale wathu ndi Yesu. Izi zitanthauza kutenga nthawi yathu yaitali ndi iye, kumanga naye m'gwirizano woona ndi wapoyera.

Mulungu watipatsa zotitsogolera zopatulika zisanu kuti zitithandize kukula mu uzimu. Zinthuzi ndi: Kuwerenga mawu ake m'baibulo, pemphero, kuchita monga mwa mawu ake, kukhalira pamodzi ndi anzathu mukupembedza, ndi kugawana nawo anzathu zomwe tapeza.

Kukhala mwa khristu sikutanthauza kuti sitingalakwitse zinthu ayi. Koma tikaphunthwa ndi kuchimwa, timaitanitsa chikhululukiro kwaYesu, ndikupitabe chitsogolo. Ife talunjikitsidwa ku njira ina yake ndipo tidziwa kuti Khristu adzakhala nafe wamoyo nthawi zonse m'mitima mwathu.

5. CHISANGALALO CHA MWAYI WACHIWIRI

Munthu wotchedwa Harold Hughes analandira maulemu ambiri mu ntchito yake yolemekezeka ngati wamkuru wakunyumba yamalamulo ku America, koma ulemu womwe udaposa onse kwa iye ndi umene analandira atangodzipereka kwa Yesu.

Harold ankawerenga ndi kuphunzira mau a Mulungu M'baibulo yekha m'chipinda chake usiku wina pamene anamva kukhudza pa bondo la mkono wake. Atatukula nkhope anaona kuti ndi ana ake a akazi awiri aang'ono, ataima mwachete pafupi naye atavala zovala zawo zogonera. Anawayang'ana iwo kwa kanthawi, anali osinthika kwambiri, ndipo anali atasowana nawo kwa nthawi yaitali chifukwa chamoyo wake wauchidakwa.

Ndiye mwana wamn'gono kwambiri, Carol, anati: "Adadi, tabwera kudzakupsopsonani kuti mugone bwino." Maso abamboyu adachita mdima. Panali patapita nthawi yaitali kuyambira pamene anatsirizira kupsopsonana nawo ana ake. Koma panopa anawanso sanaonetse mantha, anabwera m'maso mwawo mokongola ndi moyera. Bambo anabwera kunyumba tsopano.

Yesu anatipatsadi ife anthu mwayi wachiwiri. Iye amachotsa milandu yonse yochotsa chiyembekezo ndi kutitengera kuyambanso kwatsopano.

Mpulumutsi akufuna wina ali yense wa Iye abwerere kunyumba. Kodi mwavomera kuitana kwachikondi kwa Khristuku? Kulandira kukhululukidwa ndi kuyeretsedwa ndi Mulungu ndikosavuta ndi kwakuya ngati kungotambasula mikono yanu kuti mwana wanu akukhumbatireni, kukupsopsonani.

Ngati simunakhulupilirebe mwa Khristu ngati Mpulumutsi wanu, mutha kutero nthawi inoyi pongopemphera motere:

"Atate, ndiri ndi chisoni ndi moyo wanga wakale wauchimo. Zikomo putuma mwana wanu Yesu Khristu ku dziko lino lapansi kudzafa m'malo mwa ine. Yesu, chonde, mundikhulukire machimo anga ndipo mudze mukhale m'moyo wanga ndikundipulumutsa. Ndifuna mwayi wachiwiri pa moyo wanga - ndikufuna kubadwanso mwatsopano. Koposa zonse, ndifuna ndikhale pa ubale nanu tsiku ndi tsiku. Zikomo chifukwa chochita chozizwa ichi kwa ine. M'dzina la Yesu Khristu, Amen."

Pangani kufufuza kozizwitsa uku: Ife tikakonzekera kubwera, Iye amachita mbali yakupulumutsa.


M'MENE TIMALANDILIRA MOYO WATSOPANO KUCHOKERA KWA KHRISTU

(i) Timakhulipilira mwa Iye ndi kumulandira Iye ngati Mpulumutsi ndi ambuye.

(ii) Timakhazikitsa ubale ndi Iye. (Nthawi zonse kukhala ndi pemphero ndi maphunziro a Mawu ake ndizofunika kwambiri).

(iii) Khristu amagwira ntchito mwa Mzimu wake woyera kubweretsa makhalidwe ake abwino kuti alowe m'malo mwa makhalidwe athu oipa omwe amawachotsa.


 

© 2003 The Voice of Prophecy Radio Broadcast
Los Angeles, California, U.S.A.