ULALO WA KU MOYO WOKWANITSIDWA

Anapeza mafupa pambali pa denga la msasa wina wake pa chisumbu chapachokha pakati pa nyanja ya Atlantic.

Wapanyanja wopanda dzina uyu ankasunga zonse za zolembedwa pa miyezi yake inayi yakukhala panyanja. Ananyamuka ulendo wake wapanyanja pa chisumbu cha kukwera ndi gulu la panyanja la ma Dutch muchaka cha 1725 chifukwa cha mulandu womwe sukutchulidwa. Posakhalitsa chifukwa cha ludzu lalikulu lamadzi, anafika pomwa mwazi wa a fulu a m'madzi. Kuvutika kwake kunali kwakukulu, koma chomupweteka kwambiri mwa zonse, monga mwa kulemba kwake, akuti unali: mlandu wa tchimo lake lalikuru.

Analemba mawu owawa ngati awa: "Kodi ndi kuwawa kotani komwe ochimwitsitsa amamva atasiyana nayo njira yachilungamo, nakondwera kuonjezera chiwerengero chaotayika". Wapanyanjayu ndikudzipatula kwake m'gulu pa chisumbu chapaokha chija kunabwera ndi maganizo ake akuti walekananso ndi Mulungu. Ndizomwe zinampangitsa kulephera kudzigwira ndi kudzivomera pa mapeto pake.

Anthu akhala akulimbana ndi kudzilekanitsa kwa mtimaku kuyambira pomwe Adamu ndi Hava "Anabisala kwa Ambuye Mulungu mu mitengo ya M'munda muja", atatha kudya chipatso choletsedwa chija (Genesis 3:8).

Chowawa cha mumtima chatsopano cha manyazi, kumva kulakika, ndi mantha zinawapangitsa anthu oyambirira awiriwa kuthawa pamene Mulungu anawaitana. Maganizo awa, mwatsoka, akupezekanso mwa ife lero. Kodi ndi chiyani chenicheni chopangitsa kuti ife tikalekane ndi Mulungu?

"Koma zoipa zanu zakulekanitsani inu ndi Mulungu wanu; ndipo machimo anu abisa nkhope yace kwa inu." - Yesay 59:2.

Choipa chachikuluchi cholekanitsa anthu ochimwa ndi Mulungu wawo sichiri chikonzero cha Mulungu ayi: Mulungu sanamuthawe Adamu ndi Hava - iwo ndiwo adamunthawa.

1. KUKWANITSA NJALA YATHU YOBISIKA

Tchimo lisadaononge chithunzichi, Adamu ndi Hava anali mchisangalalo cha ubale ndi Mlengi wawo m'munda wokongola kwambiri wa Edeni komwe kunali kwao. Mwatsoka, anatenga bodza lonyengerera la Satana loti iwo adzakhala ndi nzeru ngati Mulungu, lomwe linaphwanya mgwirizano wokhulupirirana ndi wowapangayo (Genesis 3).

Atachotsedwa m'munda wa Edeni, Adamu ndi Hava anakhala moyo wowawa kunja kwa mundawo - kuberekana, ndi kulima mnthaka tsopano kunadzetsa mwazi, thukuta ndi misozi. Ubale wawo ndi Mulungu utasweka, anapezeka ndi zilakolako zosakwanitsika ndi zilandiro zowawa - undekha wa tchimo.

Kuyambira pamene Adamu ndi Hava adagalukira pachiyambi, "Onse" (Mtundu wonse wa anthu) unagwa mundondomeko yomweyi ya tchimo nakhala nawo mu mzere woti adzafa, chomwe chiri mphotho yake ya tchimo.

"Chifukwa chake monga uchimo unalowa m'dziko lapansi mwa munthu m'modzi, ndi imfa mwa uchimo, CHOTERO IMFA INAFIKIRA ANTHU ONSE, Chifukwa kuti onse ANACHIMWA." - Aroma 5:12.

Tonse tidakhala nawo machitidwe a njala ya zofuna za mtima pa zomwe tidataya, kufunafuna chitetezo chokhacho chomwe Mulungu yekha angapereke. Nthawi zambiri timafuna kudzikwaniritsa pogula zambiri zochitira maphwando, pofuna kukwera m'maudindo pa ntchito, kapena kuthetsa njala zathu ndi a vinyo osasa, mankhwala osokeneza bongo ndi madama. Koma zonsezi zisonyeza makhalidwe athu osoweka Mulungu. Palibenso machiritso ena ku izi oposa kupeza nawo chikondi chake m'moyo wathu.

"Inu... pankhope panu pali chimwemwe chokwanira; m'dzanja lanu lamanja muli zokondweretsa zomka muyaya." - Masalimo 16:11.

2. KULUZANITSA PHANGA LALIKURU LA TCHIMO NDI IMFA

Sianthu okha amene amaoneka osungulumwa chifukwa cha tchimo. Mtima wa Mulungu unapwetekanso panthawi yomwe Adamu ndi Hava adamufulatira Iye. Ndiponso Iye amamvabe chisoni ndi matsoka a munthu. Mulungu ndi wolola ndi wofunitsitsa kukhutitsa zofuna zathu zobisika ndi kupoletsa mabala a kusweka kwa maganizo a mumtima mwathu. Iye sanakwanitsidwe ndi kuona mwachisoni kokha pa phanga lalikulu limene lalekanitsa ife ndi Iye ayi. Mulungu anatsimikiza kukhala ulalo pakati pa phangali ndi imfa.

"Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi kotero kuti anapatsa mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira Iye asatayike , koma akhale nawo moyo wosatha. Pakuti Mulungu sanafuna mwana wake kudziko lapansi, kuti akaweruze dziko lapansi, koma kuti dziko lapansi, likapulumutsidwe ndi Iye." - Yohane 3:16, 17.

Mulungu anapereka mwana wake, ndipo Yesu anapereka moyo wake ngati nsembe ya tchimo, kulipira imfa iye mwini. Moyo wake, imfa yake, ndi kuuka kwake kunapangitsa kuti tchimo litha kukhululukidwa ndi kupulumutsa wochimwayo mopanda kulichepetsa tchimolo; ndipo dziko lapansi linalandira chitsanzo cha khalidwe lake lenileni la Khristu ndi Satana.

Ulalo wa thupi lotundudzidwa, lokha mwazi wa Yesu Khristu, limakokera anthu kuchokera ku misampha ya tchimo.

Chikondi chimakwirira phangali, kuwapangitsa onse okhulupirira mwa Khristu ngati Ambuye ndi Mpulumutsi kuyenda m'moyo wosatha.

2. MFUNDO ZISANU NDI ZIWIRI ZOFUNIKA KUZIDZIWA ZOKHUDZA YESU

Mfundozitu sizoona kwa munthu aliyense amene adakhalako:

1. YESU ANACHOKERA KUMWAMBA KUDZA PADZIKO LAPANSI
Kodi Yesu amati wakhala zaka zingati?

"Asanabadwe Abrahamu Ine ndiripo." - Yohane 8:59.

Yesu analidziwitsa dziko lapansi: "Ndine"! Ndakhalako kuyambira kale ndipo ndidzakhalakobe. Ngakhale Yesu anabadwira mwa mayi wa umunthu (Mateyu 1:22, 23) Iye ndi Mulungu - Mulungu mwa munthu.

Dwight L Moody, yemwe ndi Billy Graham wa mu zaka za mazana khumi ndi anayi, (19th Century) nthawi ina ananenapo za umunthu wa Yesu Khristu kuti, " Ikanakhala nsembe yaikuru kuti Yesu abwere ndikubadwira muchobadwira cha siliva, nasamalidwa ndi angelo, nadyetseredwa ndi ng'ombe ya golide. koma mlengi wa kumwamba ndi dziko lapansi anadza nakhala ndi thupi la umunthu, nabadwira mkhola, mwa makolo osauka ndi munyengo ndi malo oipa.

M'ngelo anamuuza Yosefe pa nthawi ya kubadwa kwa Yesu:

"Ndipo (Mariya) adzabala mwana wamwamuna, ndipo udzamucha dzina lake Yesu, pakuti IYEYO ADZAPULUMUTSA ANTHU ACHE KU MACHIMO AO." - Mateyu 1:21.

Yesu, Mlengi wa dziko lapansi (Yohane 1:1-3, 14), anali wolola kudza ku dziko lapansi kudzapulumutsa ife kumachimo ndi imfa.

(2) YESU ANAKHALA MOYO WOSACHIMWA
"Yesu Mwana wa Mulungu,... wayesedwa m'zonse monga momwe ife - koma wopanda uchimo." - Aheberi 4:14, 15.

Mulungu anachita zambiri zoposa kungotiuza ife za kuchoka ku moyowu wa tchimo kupita ku moyo wokwanitsidwa. Pokhala nafe ngati munthu, Yesu anaupanga moyo wopanda tchimo, ndiwosiririka moti palibenso ulaliki womwe ukanatha kuonetsera izi motere.

Satana, mdani wa Khristu, anakonza chiwembu mu moyo wake wonse wa Yesu kuti amugwetse Iye mu tchimo. Mu chipululu, Satana anachita mbali yake yonse yantchito yake yoopsya yothetsa ulemu wake wa Khristu (Mateyu 4:1-11). Mu Getseman, Iye asanapachikidwe, mayesero anamfikira kwakukuru kufikira kuturutsa thukuta la mwazi (Luka 22:44).

Koma Khristu anaima nji! ku mayesero onse mdirekezi anamukonzera -
"Wopanda kuchimwapo". Chifukwa chakuti Yesu anakumana nawo uthunthu wonse wa mavuto ndi mayesero, amamvetsetsa za kuvutika kwathu poyesetsa. Amatha "Kumva nafe chisoni pa kufooka kwathu" (Aheberi 4:15).

Zinatheka bwanji kuti Yesu akhale moyo wopanda tchimo?

"Ameneyo sanadziwa uchimo anamuyesera uchimo m'malo mwathu; kuti ife tikhale chilungamo cha Mulungu mwa Iye." - 2 Akorinto 5:21.

(3) YESU ANAFA KUTI ACHOTSE TCHIMO
Kodi ndi anthu angati amene anachimwa?

"Pakuti onse anachimwa, naperewera pa ulemerero wa Mulungu." - Aroma 3:23.

Nanga mphotho yake ya uchimo ndi chiyani?

"Pakuti mphotho yake ya uchimo ndi IMFA, koma mphatso yaulere ya Mulungu ndiyo moyo wosatha mwa Khristu Yesu Ambuye wathu." - Aroma 6:23.

CHIFUKWA CHIYANI YESU ANAFA?

"Taonani, Mwana Wankhosa wa Mulungu, amene ACHOTSA MACHIMO a dziko lonse lapansi" (Yohane 1:29).

Tonse tinachimwa ndipo tiyenera imfa yosatha, koma Yesu anafa m'malo mwathu. Anasanduka "Tchimo kwa Iye". Analipira dipo lathu. Kufa kwake kuli mphatso, ndi "MPHATSO ya Mulungu ndi moyo WAMUYAYA kwa Khristu Yesu Ambuye wathu" (Aroma 6:23).

Yesu anasiya ungwiro wake, moyo wake wachilungamo ngati mphatso yachikondi kwa ife. Chikondi chotere ndichoti munthu sangachimvetsetse. Ndipo chifukwa cha imfa yakeyi "tiri ndi MTENDERE ndi Mulungu" (Aroma 5:1).

(4) YESU ANAUKA KWA AKUFA
Imfa ya Yesu pa mtanda sanali mapeto ambiri yake yodabwitsa ayi. Sakanakhala wakufa nakhalabe Mpulumutsi wathu.

"Ndipo ngati Khristu sanaukitsidwa, chikhulupiriro chanu chiri chopanda pache; muli chikhalire m'machimo anu. Chifukwa chake iwonso akugona mwa Khristu anatayika." - 1 Akorinto 15:17, 18.

Muhamadi ndi Buda aphunzitsa ziphunzitso zina zazikuru ku dziko lapansi. Ndipo akhudza miyoyo zikwizikwi ya anthu ndi uthenga wawo, koma alibe mphamvu zodabwitsa zakupereka moyo. Ndichifukwa onsewa adakali m'manda mwawo.

Ndi chifukwa chiyani Yesu anauka m'manda pa tsiku lachitatu kuchokera pomwe anafa,nanga ndi lonjezano liti lomwe akufuna kupanga kwa ife?

"Popeza Ine ndiri ndi moyo inunso mudzakhala ndi moyo." - Yohane 14:19.

Yesu ali wa moyo! Chifukwa ali ndi mphamvu zogonjetsera imfa ndi kupereka moyo womwe uli wamphumphu ndi wosatha. Adzakhala mu mtima mwathu ngati timuitana. Khristu woukitsidwayo alipo lero kukumana ndi zosowa zathu.

"Ine ndiri pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimariziro cha nthawi ya pansi pano." - Mateyu 28:20.

Amuna ndi akazi padziko lonse lapansi akugawana nawo nthanoyi ya m'mene Khristu wawachotsera kuwapulumutsa ndi kuwamasula ku zizolowezi zoipa za moyo uno.

M'modzi wa aphunzi akale adalemba mawu awa oyamikira pa limodzi la mapepala ake a mayankho: "Ndinali chidakwa. Tsiku lina ndiri chiledzelere, ndinapeza chikalata cholengeza za maphunziro anu a baibulo mu malo oyenda madzi. Ndinalitenga pepalalo, nandilembapo, nandiyamba kulandira chidziwitso choona choyamba cha Khristu. Nditangotsiriza maphunzirowa ndinapereka moyo wanga kwa Mulungu ndikusiya moyo wauchidakwawo".

Pamene Yesu anatenga ulamuliro wa moyo wa munthuyu, mphamvu ina yake yatsopano inampatsa Iye mphamvu yogonjetsera zizolowezi zake. Pakuti Khristu ndi Mpulumutsi woukitsidwa, adzapulumutsa aliyense wodza kwa Iye kufuna chithandizo.

(5) YESU ANAKWERA KUNKA KUMWAMBA
Yesu atangouka kwa akufa asanakwere kubwerera kwa Atate (Machitidwe 1:9), anapereka lonjezo iri kwa omutsatira Iye:

"Mtima wanu usabvutike; mukhulupirira Mulungu, khulupirirani inenso. M'nyumba ya Atate wanga alimo malo okhalamo ambiri;... ndipita KUKAKONZERANI INU MALO. Ndipo ngati ndipita kukakonzera inu malo... ndidzabweranso ndipo ndidzalandira inu kwa Ine ndekha... kumene kuli ineko. Mukakhale inunso." - Yohane 14:1-3.

(6) YESU AKUTUMIKIRA MONGA WANSEMBE WAKUMWAMBA
Yesu nthawi zonse amayesetsa kufufuza kupeza motikonzetsera malo kumwamba.

"Potero kudamuyenera kufanizidwa ndi abale m'zonse, Kuti akadzakhala mkulu wa ansenbe wachifundo ndi wokhulupirika m'zinthu za kwa Mulungu, kuti apereke dipo la zoipa za anthu. pakuti popeza adamva zowawa, poyesedwa yekha, akhoza kuthandiza iwo amene ayesedwa." - Aheberi 2:17-18.

Yesu anadza ku dziko lapansi "Kudzapereka dipo lake la chimo za anthu". Ndikuwapulumutsa iwo kuchokera ku Zisoni za ukapolo wa machimowo. Anafa kutipulumutsa kuti akathetse zomwe ziyambitsa tchimo, kuzunzika, ndi imfa pomuphwanya mdierekezi.

Yesu, wansembe wathu wamkulu "aNapangidwa mu zonse monga abale ake". Ndipo pano akuonekera pamaso pa Atate mmalo mwathu ngati wotiimirira. Yesu yemweyo yemwe anadalitsa ana anapulumutsa ndi kumukonzanso mayi wogwidwa ndi chigololo, nakhululukira mbala yofa pamtanda; akugwira ntchito panopa kumwamba kukwaniritsa zosowa zathu "kuthandiza iwo amene akuyesedwa".

(7) YESU ADZABWERANSO YESU ASANABWERERE KUNKA KUMWAMBA, ANALONJEZA CHIYANI?

"Ndipo ngati ndipita kukakonzera inu malo, 'ndidzabweranso' ndipo ndidzalandira inu kwa Ine ndekha, kuti kumene kuli Ineko, mukakhale inunso." - Yohane 14:3.

Yesu podzabwera, adzatimasula ife ku chimo, matenda, matsoka ndi imfa zomwe zabvutitsa dziko lapansi. Ndipo adzatilandira ife ku dziko latsopano chisangalalo cha muyaya ndi moyo wosafa.

4. CHIKONDI CHOSALEPHERA

Nthano ikunenedwa ya ukwati womwe unakonzedwa ku Taiwani pakati pa U Long ndi msungwana dzina lake "Golden Flower". Pamene U Long anavundukula chofunda chakumutu cha mkwatibwi wake utatha mwambo wokwatitsidwa, anazizwa modabwitsika kuona kuti nkhope yonse ya mkaziyo inakutidwa ndi zipsera za nthomba.

Zitatha choncho, U Long analibe nayenso chidwi mkaziyo. Anayesetsa mkaziyo kumukondweretsa U Long pogwira ntchito molimba panyumba ndi chiyembekezo choti mwamuna wake ankonde momwe aliri. Koma iye anakhalabe wosayamikira machitidwe a mkazi wakeyu.

Patatha zaka khumi ndi ziwiri a banja lotereli, U long anayamba kusaonetsetsa bwino. Madotolo pumuyeza adamuuza iye kuti tsiku lina adzakhala wa khungu ngati sangathe kukaikitsa choonera china cha mdisomo chatsopano. Koma kuikitsako ndi ntchito yakeyo zinali zofuna ndalama zambiri koposa komanso panali mndandanda wa anthu ambiri ofuna chithandizo chomwechi asanafike iye.

Mkazi wake, Golden Flower anayamba kugwira ntchito nthawi yaitali patsiku kupanga zisoti za mulaza kuti apeze ndalama zoonjezera. Tsiku lina, U Long anauzidwa kuti wina wake ali ndi chamdiso chomwe iye akuchifuna chija anathamangira kuchipatala kuja komwe anakamupanga opereshoni.

Atachira, adadzikakamiza mwazifukwa kuti aonane ndi mkazi wake kuti amuthokoze iye poyesetsa kupeza ndalama. Pamene mkaziyo anatukula mutu wake kuti amuyang'ane mwamuna wake anamuona iye wakhungu, maso opanda kanthu, chiwalo chofunika chija choyera cha diso chitachoka, akuthatha. Atakhudzidwa ndi chisoni, anabisa nkhope yake nayamba kulira. Kwa nthawi yoyamba U Long anaitana monong'ona dzina la mkazi wake : Golden Flower.

Yesu akufufuza ubale ndi iwo amene amkayika Iye namutsutsa kwa nthawi yaitali; Akufuna ife kuti pamapeto pake tiitane monong'ona dzina lake ndi kulitchula ngati mpulumutsi wathu. Iye anali wolola kupereka moyo wake nsembe osati maso ake okha ayi koma thupi lake lonse kuonetsera chikondi chake chosalephera. Chikondi chake ndi champhamvu koposa kotero kuti Khristu "anadza ku dziko kudzapulumutsa wochimwa" (1 Timoteo 1:15).

Nsembe yaikulu ya Khristu yabweretsa ulalo womwe walunzanitsa kusiyana maganizo kwathu, komwe kwakuta kupunduka kwathu. Kodi inu panokha, mwapeza kuti iye akufuna kukudutsitsani inu dzenjeli kuti mugwe m'manja ake? Mungavomere ndi kupemphera kuti, "Yesu, ndimakukondani. Zikomo chifukwa cha chikondi chanu chodzipereka nacho nsembe. Idzani mu mtima mwanga ndi kundipulumutsa ine ndense, kwathunthu ndi kwamuyaya?"


YESU

Anadza ngati Mulungu mwa Munthu
Anakhala moyo wopanda tchimo mmalo mwa ife
Anafera zochimwa zathu
Anauka kutiomboloa ife kuimfa
Anakwera kumwamba kukatikonzera mudzi wokhalako
Akutumikira tsiku ndi tsiku ngati wansembe wanthu wamkuru
Akubwera posachedwa kudzatitenga ife kuti tikakhale ndi Iye kwa muyaya


 

© 2003 The Voice of Prophecy Radio Broadcast
Los Angeles, California, U.S.A.