KODI MOYO WANGA NGOFUNIKA
PAMASO PA MULUNGU

Nthawi zina dziko limaoneka labwino ngati Paradizo. Ukadzuka m'mawa, kupuma kupyolera pa zenera mmene dzuwa likuwalira mosangalatsa loonekera mmitengo, tsamba ndi tsamba la mtengo. Nthawi zina, zimapangitsa moyo kuoneka wofunika ndi wabwino: Nkhope ya bwenzi lokondeka amene akutsazikana nawe, tinyimbo tongodutsa tomveka mogwirizana ndi nthawi yace, komanso chikoka chosayembekezeka cha mwana wang'ono.

Koma nthawi zina, dziko limaoneka ngati malo atsoka. Ukadzuka mmawa nuwerenga nyuzipepa ndi mitu yake yonena za anthu oipsa anzao ataombera malo kupangitsa anthu kulumala; kukhala akhungu ndi ana omwe; komanso wakupha wina akupha munthu wake wachikhumi; komanso kwina njala ndi kusefukira kwa madzi kapena nkhondo ndi chivomerezi zitasautsa. Izi ndi nthawi zimene chirichonse chimakhala chopanda pake, palibe chimaoneka chabwino.

Nanga zonsezi zitanthauzanji? Tingapezepo zinthu zenizeni mu dziko lodabwitsali ndi loopsali? Kodi tiriko chifukwa chiyani? Kodi moyo wanga uli wofunika kwa Mulungu kapena ndangokhala kanthu kena kake kakang'ono mu chimakina chachikulu kwambiri moti sindingaonekere?

1. MULUNGU ANALENGA DZIKO LANGWIRO

Mulungu ndi Mlengi; katswiri wolikonza ndi kuliona dziko m'mene lingakhalire asanalipange kuona kuyambira ku nyenyezi yaikulu mpaka ku phiko la gulugufe.

"Zakumwamba zinalengedwa ndi mau a Yehova; ndipo ndi mpweya wa m'kamwa mwace khamu lao lonse…. Pakuti ananena, ndipo chinachitidwa; Analamulira, ndipo chinakhazikika." - Masalimo 33:6-9.

Mulungu amangolankhula kokha ndipo zinthu zonse zinamumvera m'chifuniro cace.

2. MASIKU ASANU NDI LIMODZI KUPANGA DZIKO LATHU

"Chifukwa masiku asanu ndi limodzi Yehova adamaliza zakumwamba ndi zapansi, ndi nyanja, ndi zinthu zonse ziri m'menemo, napumula tsiku lacisanu ndi chiwiri, chifukwa chache Yehova anadalitsa tsiku la Sabata kuti likhale lopatulika." - Eksodo 20:11.

Mulungu wamphamvu zonse ndi wamuyaya akanatha kulilenga dziko lonse mukamphindi "munthawi yakupuma kamodzi kwa Iye" Koma Iye anasankha kuigwira ntchitoyi masiku asanu ndi limodzi, mphindi zisanu ndi limodzi kapena kucheperapo zinalinso zokwanira kwa Iye. Mutu woyambirira mu Bukhu lopatulika, Genesis 1, likulongosola zomwe Mulungu analenga pa tsiku lirilonse la pamulungu.

Kodi chomalizira chofunika ndi chiti chomwe iye adalenga tsiku lachisanu ndi chimodzi?

"MULUNGU NDIPO ADALENGA MUNTHU M'CHIFANIZO CHAKE M'CHIFANIZO CHA MULUNGU ADAMLENGA IYE, ADALENGA IWO MWAMUNA NDI MKAZI." - Genesis 1:27.

Mulungu adaganiza zolenga munthu wofanana ndi Iye yemwe akadatha kuganiza, kumva ndi kukonda, Munthu aliyense wapangidwa "m'chifanizo" cha Mulungu.

Pofika tsiku lachisanu ndi chimodzi, dziko linali litadzala ndi zomera ndi nyama, ndipo Mulungu anaonetsera cholengedwa chake chofunikira monga mwa Genesis 2:7, Mulungu wamphamvu zonse adampanga Adamu ndi thupi lake kuchokera kudongo la panthaka. Ndipo pamene Iye anauziramo "mpweya wa moyo" mu mfuno zake, munthuyu anakhala "wamoyo" - kutanthauza kuti anasandulika kukhala wamoyo. Mulungu anapanga munthu woyambayo Adamu m'chifanizo chake; Adamu, kutanthauza 'Mwamuna' ndi mkazi woyamba Hava, kutanthauza "Umoyo" (2:20; 3:20). Mlengi wokonda anaona kufunika kwa kukhala ndi wothandizana naye pa umunthu.

Chopangidwa mwatsopano ndi dzanja la Mulungu, Adamu ndi Hava, onse anaonetsadi chifanizo cha Mulungu. Mulungu akanatha kuwapanga iwo ngati ma roboti kuti azingowayendetsa m'munda wa Edeni mmene Iye afunira ndi kuwauza kukweza mau awo motamanda Iye. Koma Mulungu anafuna zambiri; Chiyanjano chenicheni. Maroboti kapena zidole za magetsi zitha kumwetulira, kuyankhula, ngakhale kutsuka mbale ngati mwawalamula; koma sizingathe kukonda.

Mulungu anatilenga m'chifanizo chake, ndi ufulu wonse wakuganiza ndi kusankha, kukumbukira, kumvetsetsa ndi kukonda mwatokha. Adamu ndi Hava anali ana a Mulungu, ndi ofunikira ndi okondedwa ndi iye.


MULUNGU (SABATA) WAKULENGA

Tsiku loyamba; Kuwala, ndondomeko ya usana ndi usiku.
Tsiku lachiwiri; Mlengalenga wa dziko lapansi.
Tsiku lachitatu; Dziko louma ndi zomera.
Tsiku lachinayi; Dzuwa ndi mwezi zinaoneka.
Tsiku lachisanu; Mbalame ndi nsomba.
Tsiku lachisanu ndi chimodzi; Nyama zakumtunda ndi Munthu.
Tsiku lachisanu ndi chiwiri; Sabata.


3. CHOIPA CHIDZA KU DZIKO LANGWIRO

Adamu ndi Hava anali ndi chirichonse chowapanga iwo kukhala okondwa. Anakondwa ndi kusangalatsidwa ndi thanzi lawo lathupi ndi maganizo, kukhala m'munda wokongola, nyumba ya dziko lopanda banga (Genesis 2:8; 1:28-31). Mulungu anawalonjeza iwo ana ndi mphamvu ya maganizo a kulenga, ndi kupeza chikwaniritso mu ntchito za manja awo (Genesis 1:28; 2:15). Anaonana naye Mulungu maso ndi maso; popanda kalikonse kobweretsa chidandaulo, mantha, matenda, kuwasokoneza mu masiku awo abwinowo.

Nanga dziko linasinthika bwanji mwachangu kukhala malo a mazunzo ndi matsoka? Mutu wachiwiri ndi wachitatu wa bukhu la Genesis ukunena nthano yonse ya m'mene chimo linalowera mu dziko lapansi. Werengani panokha munthawi yanu. Koma pano tinena mwa chidule za nthanoyi.

Nthawi imene Mulungu anatha kupanga dziko langwiro, mdierekezi anabwera m'munda wa Edeni kudzamuyesa Adamu ndi Hava kuti asamvere Mulungu Mlengi wawo. Koma Mulungu anachepetsa ukulu wa yeso la mdierekezili ku mtengo umodzi wa mmundamo, "Mtengo wakudziwitsa zabwino ndi zoipa" Ndipo Iye anawachenjeza awiriwo kuti asaukhudze ndipo asadye zipatso zake; apo ayi adzafa akadzadya.

Koma tsiku lina Hava ankayendayenda mouzungulira mtengo woletsedwawu. Pomwepo Satana anapezerapo mwayi wogwira ntchito yake. Anaonetsa kwa Hava kuti Mulungu wanama kwa iwo ndipo kuti akadzadya za mumtengowo adzakhala odziwa zabwino ndi zoipa, nakhala ndi nzeru ngati za Mulunguyo. Mwatsoka Hava ndi Adamu, omwe panthawiyi ankadziwa zabwino zokha zokha, anamulola Satana kuwanyenga, ndipo anadyadi zipatso za mumtengo woletsedwawo - kuphwanya ubale wokhulupilirana ndi kumvera, Mulungu.

Mulungu anawakonzetsera Adamu ndi Hava "kulamulira" pa dziko lonse lapansi ngati adindo a zolengedwa zonse za Mulungu ndi ntchito yake (Genesis 1:26). Koma chifukwa iwo anaphwanya chikhulupiliro chawo ndi Mulungu, nasankha Satana ngati mtsogoleri wawo watsopano, iwo awiriwa anataya ulamuliro wawo. Lero Mdierekezi walitenga dziko lapansi ngati lake ndipo akuyesetsa kuwaika anthu mu ukapolo.

Nthawi zambiri timapezeka tiri odzikonda, ankhanza, ngakhale pamene sitifuna kukhala otero. Nanga ndichifukwa chiyani? Ndichifukwa chakuti, mdani wosaonekayo, Satana akugwira ntchito yake mwa anthu kuti alephere m'chikhalidwe.

Pamene muwerenga mutu wachitatu wa bukhu la Genesis, mupeza kuti chimo linapangitsa Adamu ndi Hava kubisala pamaso pa Mulungu chifukwa cha mantha. Chimo linakhudza chilengedwe chonse. Mungalipeze muzomera ndi maluwa ake, kubereka kwa ana kunasanduka chinthu chowawa. Matenda adayamba kugwa nthawi ndi nthawi. Dumbo, chikhalidwe cha unyama, kaduka zinakulirabe pakati pa mtundu wa anthu, ndipo zinawapangitsa kuoneka ozunzika. Choopsa cha zonse chomwe chinadza ndi utchimo ndicho imfa!

4. KODI MDIYEREKEZI AMENEYU NDI NDANI KUTI MPAKA AONONGE DZIKO LATHU LAPANSI NDI TCHIMO?

"Iyeyu anali wambanda kuyambira pachiyambi,… pakuti mwa iye mulibe choonadi. Pamene alankhula bodza, alankhula za mwini wake; pakuti ali wabodza, ndi ATATE WACHE WA BODZA." - Yohane 8:44.

Malinga ndikufotokoza kwa Yesu, Mdierekezi ndiye chiyambitso cha tchimo mdziko lapansi, 'tate' wa tchimo mongatu kupha ndi bodza.
Thomas Carlyle, woganiza mwakuya pachinenero cha chingerezi anamtenga Ralph Waldo Emerson tsiku lina ndikuyenda naye mu misewu yoipitsitsa ya kummawa kwa mzinda wa London. Mmene amayenda, amayang'anitsitsa mwakachetechete zoipa ndi zambanda zonse zomwe zimachitika mowazungulira; pamapeto pake Carlyle anafunsa "ukukhulupilira mwa Satana mdiyerekezi tsopano"?

5. KODI MULUNGU ADAMULENGA MDIEREKEZI?

Ayi! Mulungu wabwino sakanatha kulenga mdierekezi komabe Baibulo lopatulika likunena kuti Mdierekezi ndi angelo ake adawanyengawo, anataya malo awo kumwamba nabwera padziko lathuli lapansi
"ndipo munali NKHONDO M'MWAMBA. Mikayeli ndi angelo ache akuchita nkhondo ndi chinjoka; CHINJOKANSO NDI ANGELO AKE chinachita nkhondo; ndipo sichinalakika, ndipo SANAPEZEKANSO MALO AO M'MWAMBA. Ndipo chinaponyedwa pansi chinjoka chachikuru, njoka yokalambayo, iye wochedwa mdierekezi ndi satana, wonyenga wa dziko lonse, chinaponyedwa pansi kudziko, ndi angelo ake anaponyedwa naye pamodzi." - Chivumbulutso 12:7-9.

Nanga Mdierekezi adapezekako bwanji kumwamba poyambirira?

"Unali KERUBI WODZODZEDWA WAKUPHIMBA, ndipo ndinakuika unali pa phiri lopatulika la Mulungu… UNALI WANGWIRO M'NJIRA ZAKO CHILENGEDWERE IWE MPAKA CHINAPEZEKA MWA IWE CHOSALUNGAMA." - Ezekiel: 28:14, 15.

Mulungu sanalenge mdierekezi ayi, koma adalenga Lusifala, m'ngelo wangwiro, m'modzi waotsogolera angelo kumwamba, oima pafupi ndi mpando wa Mulungu. Koma tsono anachimwa - "chosalungama chinapezeka mwa iye." Woponyedwa pochotsedwa kumwamba, naonekera kwa Adamu ndi Hava ngati bwenzi, anasandulika m'dani woopsetsetsa wa munthu.

6. CHIFUKWA NINJI LUSIFALA, M'NGELO WANGWIRO ADACHIMWA?

"WAGWADI KUCHOKERA KUMWAMBA, iwe nthanda, mwana wa m'banda kucha! WAGWETSEDWA PANSI, IWE WOLEFULA … ndipo iwe unati mumtima mwako 'ndidzakwera kumwamba, ndidzakweza mpando wanga wa chifumu pamwamba pa nyenyezi za Mulungu; NDIDZAFANANA NDIWAM'MWAMBAMWAMBA." - Yesaya 14:12-14.

Munthu yemwe anasandulika mdierekezi adali wotchedwa Lusifala pachiyambi, kutanthauza "nyenyezi ya tsiku" kapena "uyo wowala." Mumtima mwa m'ngeloyu uchabe ndi zikhumbo za moyo zinalowa m'malo mwa kudzipeleka kwake kwa Mulungu. Mbewu ya kudzikuza inakula mwa iye nibala zipatso zofuna kutenga malo a Mulungu. Lusifala anayesetsa ndi mphamvu zake zonse ponyengelera ena a kumwambako. Nzosavuta kumuganizira Satana akutsutsana ndi Mulungu pankhani yoti Mulunguyo wawabisira zina zomwe anayenera kuzidziwanso, komanso kuti malamulo ake ndi okhwima ndipo Iye ndi Mulungu wosasamala. Anamutsutsa uyo amene khalidwe lake liri kutanthauzira chikondi.

Kodi mkangano wa kumwamba unatha bwanji? "unadzikuza mtima chifukwa cha kukongola kwako,… ndakugwetsa pansi."

Kunyada kusanduliza mkulu wa angelo kukhala Satana Mdierekezi, ndipo pofuna kuchinjiriza ufulu ndi mgwirizano wa kumwamba, iye satanayo ndi limodzi la magawo atatu la angelo linayenera kuchotsedwa (Chivumbulutso 12:4, 7-9).

7. KODI MWINI WAKE WA TCHIMO NDANI?

Kodi bwanji Mulungu sanalenge anthu oti sangachimwe? Akanatero, sikunakhala vuto la choipa chiri chonse m'dziko lathu. Koma Mulungu amafuna anthu amene angakhale mchiyanjano chomvetsetsa. Choncho "Iye (Mulungu) analenga munthu mchifanizo chake" (Genesis 1:27). Izi zikutanthauza kuti tiri ndi ufulu ndikudziyankhira pa machitidwe athu onse. Titha kusankha kumkonda Mulungu kapena ayi.

Mulungu anapereka kwa angelo ndi anthu a mbadwo uli wonse mzimu ndi mphamvu zakupanga okha chisankho.

"Mudzisankhire lero amene mudzamtumikira." - Yoswa 24:15.

Mulungu akuwabetchera anthu ake omwe adawalenga kusankha kuchita bwino chifukwa choona kuti "njira ya Mulungu ndi yabwino koposa," ndikusankha kuchoka ku choipa chifukwa maganizo awo akumvetsa zotsatira zake zoopsa zachoipacho. Anthu okhawo otha kuganiza ndi kusankha angathe kupeza chikondi chenicheni. Mulungu amafunitsitsa kulenga anthu omwe akanatha kuyamikira ndi kumvetsa khalidwe la Mulungu, namlandira Iye mchikondi nakhala ndi chikondi kwa ena. Mulungu amafuna kugawana nawo chikondi chake mpaka kuti anali olola koposa kulenga angelo ndi anthu a mphamvu zakusankha, chomwenso chinali chinthu choopseza mpando wake. Ankadziwa kuti nzotheka kuti tsiku lina, chimodzi cha zolengedwa zake chitha kusankha kusamvera. Satana anali woyambilira kupanga chisankho choterechi padziko lonse. Tsoka la tchimo linayamba ndi iye (Yohane 8:44; 3:8).

8. MTANDA UNAPANGITSA TCHIMO KUKHALA LOTHEKA KULIONONGA

Chifukwa chiyani Mulungu sanaononge Lusifala tchimo lake lisanafalikire ku dziko lonse? Lusifala anaonetsa kuti ulamuliro wa Mulungu unali wopanda chilungamo. Ananena mabodza okhudza Mulungu.

Mulungu akanati amuononge iye nthawi yomweyo, angelo ambiri bwenzi akumupembedza ndi mantha osatinso ndi chikondi ayi. Ichi chikanapha cholinga cha Mulungu polenga munthu; anthu amene anali ndi mwayi wakusankha pachiyambi.

Kodi aliyense akanadziwa bwanji kuti njira yamoyo ndiyo inali yabwino koposa? Mulungu anapatsa Satana kuti aonetse njira inayo. Ndicho chifukwa chake anapatsidwa mwayi woyesa Adamu ndi Hava.

Dziko lino lakhala poyeserapo khalidwe la Satana ndipo ufumu wake ufananizidwa motsutsana ndi makhalidwe a Mulungu ndi ufumu wake. Ndani yemwe ali wolondola? Ndani amene tingamukhulupiliredi?

Lusifala analitu wonyengadi mpaka kuti patenga nthawi yaitali kuti anthu a dziko lapansi adziwe m'mene njira iliri yoononga. Koma pang'ono ndi pang'ono munthu aliyense adzaona kuti "mphotho yake ya uchimo ndi imfa ndi kuti "mphatso yaulele yaulemelero ya Mulungu ndi moyo wosatha mwa Yesu Khristu Ambuye wathu" (Aroma 6:23).

Munthu aliyense m'dziko adzabvomereza kuti "Ntchito zanu ndizazikulu ndi zozizwitsa, Ambuye Mulungu wamphamvu yonse, njira zanu nzolungama ndi zoona, mfumu inu ya nthawi zosatha… chifukwa mitundu yonse idzadza ndizolambira pamaso panu, popeza zolungama zanu zidzaonetsedwa." - Chivumbulutso 15:3, 4.

Aliyense atatha kuona kuopsa kwa chimo ndi chionongeko chobwera ndi ziphunzitso za Satana, Mulungu adzatha kuononga Satana ndi tchimo. Iye adzayeneranso kuononga iwo amene asankha moumilira kuchita tchimo ndi kutsatira mdierekezi.

Mulungu ali wa nkhawa kuthetsa vuto la tchimo ndi kuvutika ngati timulola Iye kuti atero. Koma Iye akudikira mpaka pamene akachite izi momaliziratu, mpakanso pamene angathe kusungabe ufulu wathu wa maganizo nthawi yomweyonso kuthetsa choipa kuti chisadzaonekenso.

Mulungu walonjeza kuthetsa tchimo kwa muyaya poyeretsa kumwamba ndi pansi ndi moto. "Posunga lonjezo lakeli," titha kuona "kutsogolo kuyang'anira m'mwamba mwatsopano ndi dziko lapansi latsopano, kwao kwa olungama" (2 Petro 3:10, 13). Tchimo silidzaipsanso dziko lapansi. Zotsatira zoopsa za chimo zidzaonekera poyerayera, kuonetsera kuti kusamvera cholinga cha Mulungu kudzasonyeza kunyansa kwa muyaya. Ndani apangitsa chionongeko chomaliza cha mdierekezi ndi tchimo?

"Popeza tsono ana ndiwo a mwazi ndi nyama, Iyenso (Khristu) momwemonso adalawa nawo makhalidwe omwewo kuti mwa imfa akamuononge iye amene anali nayo mphamvu ya imfa, ndiye m'dierekezi, nakamasule iwo onse amene, chifukwa chakuopa imfa, m'moyo wawo wonse adamangidwa ukapolo." - Ahebri 2:14, 15.

Pamtanda, Angelo ndi maiko osagwawo anamuona satana m'mene analiri, wonyenga, wabodza, wakupha . Apa anaonetsa khalidwe lake lenileni powamemeza anthu amuna kupha mwana wa Mulungu wosalakwa.

Anthu onse okhala mdziko lapansi anaona m'mene tchimo liriri lopanda tanthauzo ndi lankhanza. Mtanda unavumbulutsa zolinga za satana ndi onse opitiriza mu uchimo, onse adzavomereza kuti Mulungu ndi wa chilungamo.

Imfa ya Yesu pamtanda inaonetsera poyera zolinga zenizeni za satana pamaso pa anthu onse olengedwa (Yohane 12:31, 32).

Mtandanso ukutionetsera m'mene Khristu aliri Mpulumutsi wa dziko. Pa Gologota, mphamvu ya chikondi cha Mulungu inaonekera motsutsana ndithu ndi chikondi cha pa mphamvu. Mtanda unaonetseratu mopanda kukaika kuti ndi chikondi cha kudzipereka nsembe chomwe chimamulimbikitsa Mulungu pa kuthana naye satana, tchimo, ndi amuna ndi akazi ochita tchimo.

Pamtanda, paja chionetsero cha chikondi cha Mulungu mwa Khristu chinagonjetsadi mdierekezi. Nkhondo inali pakati pa kupeza yemwe angalamulire dziko, Khristu kapena satana. Ndiponso mtandawo unaweruza kwa muyaya pa nkhondoyi ayenera kukhala Khristu basi mwa zonse.

Kodi mwapeza ubale ndi Mpulumutsi yemwe anafa kuululira inu chikondi chake chosasintha? Mukumva bwanji za Iye amene anabwera kudziko lapansi ngati munthu nafa m'malo mwanu kukupulumutsani ku zotsatira za tchimo? Mungaweramitse nkhope yanu panopa ndi kumuthokoza Yesu, ndikumupempha kuti adze kutenga moyo wanu?

 

© 2003 The Voice of Prophecy Radio Broadcast
Los Angeles, California, U.S.A.