TITHA KUKHULUPIRIRA BUKHU LOPATULIKA

Oukira kapena kuti ogalukira otchuka omwe anamiza sitima ya azungu anakapezeka ali ndi azimayi a kwawo pa chisumbu cha 'Pitcairn' ku mwera kwa Pacific, okhaokha. Linali gulu la azungu asanu ndi anayi, amuna a chi Tahiti asanu ndi m'modzi, akazi a chi Tahiti khumi ndi msungwana wa zaka khumi ndi zisanu.

M'modzi wa a panyanjawa ankadziwa kutcheza mowa ndipo chifukwa cha izi uchidakwa udaononga pa chisumbupo. Kumakhala nkhanza zoopsa chifukwa amuna ndi akazi sankachedwa kumenyana ndipo adayamba kuphana. Patatha nthawi, m'modzi yekha wa anthuwo ndiye adapezeka ali ndi moyo. Koma munthuyo, Alexander Smith adapeza Bukhu lopatulika mu limodzi lamabokosi omwe anali musitimayo.

Anayamba kuliwerenga ndikuphunzitsa kwa ena zomwe anawerengazo. Moyo wake unapezeka wosinthika, ndiponso miyoyo ya anthu omwe anawaphunzitsa aja inasinthika. Anthu a pachisumbuwa anali olekanitsidwa ndi anthu ena onse a padziko mpaka pomwe opulumutsa a chi America anawapeza muchaka cha 1808. Gulu la anthuwa linapeza anthu apachisiwa akukhala mwa chipambano, kopanda mowa, ndende, kapena uchigawenga. Bukhu lopatulika linali litawasintha anthuwo kuwachotsa ku chitaiko chadziko lapansi kifika pa chidzalo cha momwe Mulungu afunira kuti anthu adzikhalira mdziko ndipo liri mpaka lero.

Kodi Mulungu akulankhulabe ndi anthu ake kupyolera mu masamba a m'bukhu lopatulika? Inde akuterodi. M'mene ndikulemba izi, ndikuona pa mayankho omwe tatumiziridwa kuchokera kwa ophunzira bukhu lopatulika pa sukulu yathu. Pansi pake waikapo mau akuti, "Ndiri m'ndende kudikira imfa chifukwa cha mlandu womwe ndidapalamula. Ndisadayambe maphunziro a bukhu lopatulikawa, ndinali wosochera; koma pano ndiri ndi chiyembekezo ndipo ndiri ndi chikondi chatsopano.

Bukhu lopatulika liri ndi mphamvu yosinthira miyoyo ya anthu. Anthu amasintha kwambiri pamene awerenga Bukhu lopatulika.

1. M'MENE MMULUNGU AMAYANKHULIRA NDI IFE KUPYOLERA MU BUKHU LOPATULIKA

Atalenga anthu oyamba, Adamu ndi Hava; Mulungu amayankhula nawo maso ndi maso. Koma atachimwa, Mulungu nawayendera; banjali linachita chiyani? Linabisala

"Ndipo anamva mau a Yehova Mulungu ali n'kuyendayenda m'minda nthawi ya madzulo: Ndipo anabisala Adamu ndi mkazi wake pamaso pa Yehova Mulungu pakati pa mitengo ya m'munda." - Genesis 3:8.

Chimo linasokoneza kuyankhulana kwa maso ndi maso ndi Mulungu. Chimo litabwera padziko, Mulungu anayankhula bwanji kwa anthu ake?

"Pakuti Ambuye Yehova sadzachita kanthu osaulula chinsinsi chake kwa atumiki ake aneneri." - Amosi 3:7.

Mulungu sanatisiye ife mum'dima pa za moyo ndi tanthauzo lake. Kupyolera mwa aneneri ake wawaitanira kulemba ndi kunenera za Iye. Watiululira ife mayankho a mafunso akulu m'moyo.

2. KODI ANALEMBA BUKHU LOPATULIKA NDANI?

Aneneri anapereka uthenga wa Mulungu polankhula ndi kulemba akadali ndi moyo. Pamene anafa, zolembera zawo zinakhala ziripobe. Maulauli awo anachitika ndi chitsogozo cha Mulungu, kupanga Bukhu lopatulika.

Kodi nanga zolemba zawozi ndizodalilika bwanji?

"Ndikudziwa ichi poyamba, kuti palibe chinenero chalembo chitanthauzidwa pachokha, pakuti kale lonse chinenero sichinadza ndi chifuniro cha munthu, koma anthu a Mulungu, ogwidwa ndi mzimu woyera analankhula." - 2 Petro 1:20, 21.

Anthu olemba bukhu lopatulika adalemba zomwe anauziridwa ndi mzimu wa Mulungu,osati zofuna ndi zokhumba zawo ayi. Bukhuli ndi la mwini wake Mulungu.

Mubukhu lopatulika, Mulungu akutiuzamo za Iye mwini ndikutiululira za cholinga chake pa munthu ndi mtundu wake. Likuonetseranso maganizo a Mulungu m'masiku akale, ndikutitsegulira tsogolo, potiuza m'mene choipa chidzathetsedwere ndi m'mene mtendere udzabwerere pa dziko lapansi.

Kodi zonse ziri mu Bukhu lopatulika ndi uthenga wochokera kwa Mulungu?

"Lemba liri lonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa pa chiphunzitso, chitsutsano, chikonzero, chilangizo cha m'chilungamo: Kuti munthu wa Mulungu akhale woyenera, wokonzeka kuchita ntchito iri yonse yabwino." - 2 Timoteo 3:16, 17.

Bukhu lopatulika limakhudza kwambiri anthu chifukwa "zonse ziri m'menemo, ziri zouziridwa ndi Mulungu. Bukhu la Mulungu ndilouziridwa.

Aneneri analunzanitsa zomwe anaona ndi kumva ndi chilankhulidwe cha anthu, koma uthenga wao unachokera mwachindunji kwa Mulungu. Choncho, ngati mufuna kudziwa tanthauzo la moyo, werengani malembo opatulika. Kuwerengaku kudzakusinthani m'moyo wanu. Ndipo pamene muwerenga ndi pemphero, ndi pamenenso mtendere wamumtima uchulukira-chulukirabe mwa inu.

Mzimu woyera omwewo unauzira aneneri kulemba Bukhu lopatulika, umapangitsa ziphunzitso zake, uthenga wake kukhala ndi mphamvu yosinthira moyo wanu ngati mwaitana Mzimuyo kuti akhale nanu pamene muwerenga Bukhuli.

3. M'GWIRIZANO WA BUKHU LOPATULIKA

Bukhu lopatulika lapangidwa ndi mabukhu makumi asanu ndi limodzi, mphambu zisanu ndi limodzi (66). Mabukhu makumi atatu mphambu zisanu ndi zinayi (39) ndiwo a chipangano cha kale omwe anapangidwa mzaka za pakati pa 1450 BC ndi 400 BC. Mabukhu otsalawo makuni awiri mphambu zisanu ndi ziwiri (27) ndiwo a m'chipangano cha tsopano omwe anapangidwa mzaka za pakati pa AD 50 ndi AD 100.

Mneneri Mose ndiye adayamba ndi mabukhu oyambilira asanu a mu Baibulo, nthawi isanafike zaka za 1400 BC. Mtumwi Yohane analemba Bukhu lomaliza Chivumbulutso mzaka zapafupi-fupi AD 95. Mu nthawi ya zaka chikwi ndi mazana asanu (1500) pakati pa nthawi ya kulemba bukhu loyamba ndi lomaliza la mu Baibulo, pafupi-fupi olemba ena ouziridwa makumi atatu mphambu zisanu ndi zitatu (38) anaperekapo maganizo awo. Ena a iwo anali ochita malonda, ena abusa aziweto asodzi, asilikali, madokotala, alaliki, mafumu, anthu antchito ndi machitidwe osiyana-siyana m'moyo uno.

Anthu onsewatu samachita ndi maganizo wofanana ayi. Koma chozizwitsa cha zonse ndi ichi kuti: Pamene mabukhu onse makumi asanu ndi limodzi, mphambu zisanu ndi limodzi (66), ndi mitu yake chikwi zana limodzi makumi asanu ndi atatu mphambu zisanu ndi zinayi (1,189) kupanga mavesi zikwi makumi atatu ndi limodzzi makumi asanu ndi awiri mphambu zitatu (31,173) anabweretsedwa pamodzi kupezamo mgwirizano wa ngwiro wa mauthenga onse operekedwa m'menemo.

Kodi tiyerekeze kuti munthu wogogoda pa khomo la nyumba yanu, ndipo pamene mwamuuza kuti alowe, iye aika mwala wa maonekedwe osokonekera pa bwalo la chipinda chanu chochezera, nachoka osanena kanthu. Enanso alendo okwanira makumi anayi nabwera momutsatira kuchita chimodzi-modzi.

Pamene womaliza wapita, namuona modabwitsidwa kuti chifanizo chokongola chaimitsidwa pamaso panu. Ndipo namupeza kuti "okonza" zifanizo ambiri sanaonepo koma nabwera, monga anachitira, ali yense ndi mwala womwe wapanga kwayekha, wina kumwera kwa America, wina ku China, wina ku Russia, wina ku Africa, ndi mbali zina za dziko lapansi. Mukanakhala ndi maganizo anji poona kuti kulumikiza miyala yaoyo kwapanga chifanizo chokongola ngati chimenechi.

Mwina mukanaganiza kuti wina wake anatumizira aliyense muyeso weni-weni ndi maonekedwe a mwala umene ayenera kupanga.

Bukhu lopatulika lonse litibweretsera uthenga umodzi wogwirizana monga ngati chifanizo chija. M'modzi yekha ndiye anapanga maganizowa, ndiye Mulungu. Kugwirizana kwa malembo a mu Baibulo ndi umboni kwa munthu, kuti kupyolera mwa munthu, maganizo a Mulungu anauziridwa kuti alembedwe.

4. MUTHA KUKHULUPILIRA BUKHU LOPATULIKA

Kasungidwe ka Baibulo ndi kodabwitsa ndithu. Zolembedwa zoyambilira zinalembedwa pa manja, makina osindikiza mabukhu asanakhaleko. Alembi ankakopera zakalezo ndikumazigawira kwa anthu. Zikwi zikwi za zomwe anakopera kapena mbali zake zina zikupezekabe mpaka lero.

Zolembedwa za chi Hebri za chipangano chakale za mzaka za pakati pa 150 ndi 200 asanabadwe Yesu khristu zinapezeka pafupi ndi nyanja ya kufa (Dead Sea) mu chaka cha 1947. Ndizodabwitsa kuti zinthu zomwe zinakhala zaka zikwi ziwiri chilembedwere zili ndi uthenga wofanana ndi womwe uli mu chipangano chatsopano cha Baibulo lathu lero. Uwu ndi umboni wamphamvu wa m'mene Mau a Mulungu aliri mukudalirika kwake.

Poyambilira, atumwi analemba zambiri za m'chipangano chatsopano ngati makalata opita kwa Akhristu a mipingo yomwe inakhazikitsidwa Yesu atafa ndi kuuka. Pafupi-fupi makalata zikwi zinayi mazana asanu (4500) a mchipangano chatsopano kapena mbali zao zikupezeka zikuonetsedwa ku malo oonetsa zinthu zakale ndi malo owerengera mabukhu otchuka ku ulaya ndi America. Ena ndi akale kwambiri. Poyerekeza zimenezi ndi Baibulo lathu lero, tipeza kuti chipangano chatsopano chiri m'mene chinalembedwera palibe chomwe chasinthidwapo ayi.

Lero, kwapezeka kuti Bukhu lopatulika ndi zolembedwa zochokera mu Baibulo zimasulidwa mu ziyankhulo ndi m'manenedwe zoposera zikwi ziwiri, kudza makumi asanu ndi limodzi (2,060). Komanso ndi bukhu limene lagulitsidwa kwambiri pa dziko lonse lapansi. Pafupifupi kuposera mabaibulo zikwi zikwi zana ndi makumi asanu (150 million) ndi mbali zake amagulitsidwa chaka chiri chonse.

(2) Mbiri yachindunji ya Baibulo ndiyodabwitsa ndi yopatsa chidwi. Zofufuza zatsimikizira izi. Oona za mbiri apeza miyala ya dongo ndi zipilala za miyala zomwe zaonetsera maina, malo ndi zochitika zake zomwe zinalembedwa mu bukhu lopatulika lokha basi.

Mwachitsanzo, monga mwa Genesis 11:31, Abraham ndi banja lake "ndipo anaturuka pamodzi nao ku Uri wa ku Kaldayo kuti amuke (ku dziko la) kanani."

Chifukwa Baibulo lokha ndilo linena za Uri, ophunzira ambiri akhala akunena kuti mzinda umenewu sunayambe wakhalapo ayi. Ofufuza za mbiri yakale adapeza nsanja ya kachisi kumwera kwa Iraq yomwe anaifukula napezapo kuti inali ndi chonga ndowa pansi pake pomwe panalembedwa m'chinenedwe cha Igupto ndipo panali liu ili la Uri, kenaka kunapezeka chivumbulutso cha Uri ngati mzinda wa chitukuko choyambilira. Ndipo Uri ndi chimodzi mwa za mbiri yakale zotsimikizira uchindunji wa Baibulo. Mzindawu ndi zochitika zake zidaiwalika, Baibulo lokha ndilo lidasunga zonsezi mpaka pamene ofufuza za mbiri ya zinthu anatsimikizira kukhalako kwake kwa mzindawu.

(3) Kukwaniritsa mu nthawi yake kwa maulosi a Bukhu lopatulika kumatisonyeza kuti tiyenera kulikhulupilira. Mau a m'Bukhu lopatulika ali ndi maulosi ambiri a zakutsogolo zomwe tikuziona ndi maso athu zikukwaniritsidwa. Timatha kufufuza mwakuya ena mwa maulosi opatsa chidwiwa, onena za maphunziro a mtsogolo.

5. TINGALIMVETSETSE BWANJI BUKHU LOPATULIKA?

Pofufuza za mau a Mulungu, kumbukirani mfundo izi:

(1) Werengani Baibulo ndi mtima wa pemphero. Ngati mutero, kumakhaladi kuonana maso ndi maso ndi Khristu pamene muwerenga mau ake (Yohane 16:13-14).

(2) Werengani Baibulo tsiku liri lonse. Uwu ndiwo mfungulo wa mphamvu m'moyo wathu, kukumana ndi maganizo a Mulungu (Aroma 1:16).

(3) Pamene muwerenga, liloreni Baibulo lomwelo litanthauzire inu. Mufunse: Kodi wolembayu akufuna kunena chiyani? Pomvetsetsa chimene ndime yolembedwayo ikunena, titha kugwiritsa mwa nzeru, tanthauzolo mu moyo wathu lero.

(4) Werengani mutu uli wonse wa mu Baibulo paokha. Yesu anagwiritsa ntchito njira imeneyi. Kutsimikizira kuti Iye ndiye Mesiya.

"Ndipo anayamba Mose, ndi kwa aneneri onse, nawatanthauzira iwo m'malembo onse zinthu za Iye yekha." - Luke 24:27.

Posonkhanitsa zonse zomwe Baibulo linena pa mutu uli wonse, timapeza kumvetsetsa kosakaikitsa.

(5) Werengani Baibulo kuti mulandire mphamvu yokhalira mwa Khristu. Mu Ahebri 4:12, akunena za mau a Mulungu kuti ali akuthwa konse-konse. Nzoposa malembo a pa pepala chabe; koma ali chida chamoyo m'dzanja lathu polimbana ndi mayesero ku chimo.

(6) Mvetsetsani pamene Mulungu alankhula nanu mu malembo ake. Ngati munthu afuna kumvetsetsa mau omwe awerenga mu Baibulo pa mutu wina uli wonse, ayenera akhale olola kutsatira zomwe akuphunzitsidwazo (Yohane 7:17) osati zomwe anthu ena akuganiza, kapena mipingo ina ikuphunzitsira ayi.


6. BUKHU LOPATULIKA LINGASINTHE MOYO WANU

"Potsegulira mau anu paunikira; kuzindikiritsa opusa." - Masalmo 119:130.

Kuwerenga Baibulo kumalimbikitsa "kumvetsetsa" kwanu ndikukupatsani inu mphamvu yogonjetsera zizolowezi zoipa ndi zoononga; ndikukupangani inu kukula mu thupi, m'maganizo, m'makhalidwe ndi muuzimu.

Bukhu lopatulika limayankhula ndi mtima. Limachita mbali yaikulu ku zochitika mwa munthu - kubadwa, chikondi, ukwati, kukhala makolo, ndi imfa. Limachiza mabala akuya mu moyo wamunthu, tchimo ndi zotsatira zake zodzetsa chisoni.

Mau a Mulungu si bukhu la mtundu umodzi wa anthu ayi, kapena msinkhu umodzi, kapena mbadwo umodzi, kapena dziko limodzi, kapena chikhalidwe chimodzi cha anthu ayi. Ngakhale linalembedwa ku m'mawa, likudandaulira amuna ndi akazi a kumadzulo. Lifikira m'nyumba za odzichepetsa ndi nyumba zikulu-zikulu za achuma. Ana akonda nthano zake zosangalatsa.

Ziphona za m'Baibulo zilimbikitsa achinyamata. Odwala, amasiye, ndi okalamba apezamo chitonthozo ndi chiyembekezo cha moyo wabwino.

Pakuti Mulungu amagwira ntchito yake kudzera mu Baibulo, ilo liri ndi mphamvu. Limaphwanya mitima youma, ndi zovuta zamoyo, kuifewetsa ndikuidzadza ndi chikondi.

Taona Baibulo ife likusandutsa wambanda ndi wosuta modetsa nkhawa kukhala mphunzitsi woona ndi woongoka. Ndipo taona Bukhu lomweli likumuchotsa munthu pa chingwe chomwe amafuna kudzipachikapo kuti afe ndikumupatsa chiyembekezo pa kuyambanso mwatsopano. Baibulo limadzutsa chikondi pakati pa adani. Limapangitsa onyada kudzichepetsa, ndi odzikonda kukhala ochita za chifundo. Baibulo limatilimbikitsa tikafooka, kutisangalatsa pamene takhumudwa, kutitonthoza m'chisoni; kutitsogolera pamene sitikumvetsetsa, komanso kutipulumutsa pamene tathodwa. Limationetsera m'mene tiyenera kukhalira molimba mtima ndi kufa opanda mantha.

Bukhu la Mulungu, Baibulo, litha kusintha moyo wanu! Mupeza zambiri za izi momveka bwino pamene muwerengabe mopitiliza zolemba izi za "chotsogolera kupeza."

Chifukwa chiyani Baibulo linalembedwa kwa ife? Yesu akuyankha:-

"Koma zalembedwa izi (choonadi cha Baibulo) kuti mukakhulupilire kuti Yesu ndiye Khristu Mwana wa Mulungu, ndi kuti pakukhulupilira mukhale nawo moyo m'dzina lake." - Yohane 20:31.

Chifukwa chachikulu choti tikhale odziwitsitsa bwino mau opatulikawa ndi chakuti, muli zithunzi-thunzi za kwa ife za m'mene Yesu Khristu atitsimikizira ife za moyo wosatha. Poona Khristu Kupyolera mu Baibulo, tinasinthika ndikukhala pafupifupi monga Iye. Tsono bwanji osayamba tsono kufufuza ndi kupeza mphamvu za m'mau ake omwe angakupangeni kufanana ndi Yesu?

 

© 2003 The Voice of Prophecy Radio Broadcast
Los Angeles, California, U.S.A.